Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 106

Paphata pa Chichewa (b) Malo okwera. Chitsanzo: Tikafika kuchikwezako mutsika kaye. Kuchilimika: Kuchita khama. Chitsanzo: Ingochilimikani kulima, chaka chino mvula iliko! Kuchimina: Kulapa kuti sudzachitanso, kukhaula. Chitsanzo: (1) Ndachimina, sindidzayendanso osavala nsapato mumchenga. (2) Achimina kuti sadzagwiranso waya wa magetsi. Kuchimwa: Kulakwa, kuchita tchimo. Chitsanzo: Mukapanda kuchenjera ndi atsikanawa muchimwa. Kuchimwitsa: Kupereka mimba kwa mtsikana. Chitsanzo: (1) Mwana wanuyu wachimwitsa mtsikana. (2) N’chifukwa chiyani anthu amanena kuti mnyamata wachimwitsa mtsikana pomwe onsewo amakhala atachimwa. Kuchinya: (a) Kugoletsa. Chitsanzo: Anapereka mphoto kwa onse omwe anachinya. (b) Kuposa munthu. Chitsanzo: Anzathutu ndiye mwatichinya, mwamaliza kale ntchito yanu! Kuchita bwino: (a) Kukhala olemera. Chitsanzo: Banja limeneli ndi lochita bwino. (b) Kukhoza bwino. Chitsanzo: Mwanayu amachita bwino m’kalasi. (c) Kuchita zinthu molongosoka. 105