Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 104

Paphata pa Chichewa Chitsanzo: Tamubwanyuleni pakamwa watukwanayo! Kubwebwetuka: Kuyankhula mosaganiza, kulongolola. Chitsanzo: (1) Udzayerekeze kubwebwetuka pali ine, ndi- dzakubwanyula pakamwa. (2) Amakonda kubwebwetuka akaona anthu. Kubwekera: Kuyamikira kukoma kwa chinthu. Chitsanzo: Alendowa akungobwekera chilichonse. Kubwenje: Kudzenje, kuphanga. Chitsanzo: Ndalama yake yagwera kubwenje. Kubwerera kukhosi: Kufunsa kusanza, kukanika ku- meza. Chitsanzo: Chakudyachi chikundibwerera kukhosi. Kubwerera m’mbuyo: Kusiya kuchita bwino, kufooka, kulephera. Chitsanzo: (1) Abusawa ndi amene akuchititsa kuti Akhristu ambiri abwerere m’mbuyo. (2) Poyamba ankakhoza bwino m’kalasi, koma pano wabwerera m’mbuyo. Kubweza moto: (a) Kubweza mwano. Chitsanzo: Mwanayu wayamba kudziona kuti wakula moti akumabweza moto. (b) Kuugwira mtima, kuchepetsa nkwiyo. Chitsanzo: Anabweza moto anzawowo atawapepesa. Kubwibwitsa: Kuyankhula mwachibwibwi. Chitsanzo: Amati akakwiya amayamba kubwibwitsa, ke- nako amangowapulumutsa makofi. 103