Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 103

Paphata pa Chichewa Kubuka: (a) Kutchuka kwambiri, kumveka. Chitsanzo: Sindimadziwa kuti munthu amene uja angabu- ke chonchi. (b) Kuyambika. Chitsanzo: (1) Nkhaniyi inabuka mwanayu atakadikiza nsima kwawo. (2) Mavuto akabuka tizigwirana manja. (c) Kuyaka. Chitsanzo: Galimotozo zitangogundana, panabuka chimo- to choopsa. Kubulika: (a) Kuyankhula mwano. Chitsanzo: Usakadabwe pakamwa pake pakakayamba ku- bulika phunzo. (b) Kulawira kapena kudzuka mofulumira kwambiri. Chitsanzo: Ndimadabwatu kuti zatani kuti abulike kusa- nache? (c) Kutuluka mofulumira kwambiri. Chitsanzo: Mbewayo itaona kuti zavuta, inabulika. (2) Mwamuna wakubayo anabulika m’nyumba atamva mawu a mwini mkaziyo. Kubushula: Kuchotsa mimba. Chitsanzo: Atatenga mimba ali pasukulu, anangobushula. Kubwadamuka: Kuwira. Chitsanzo: Kodi madzi aja abwadamuka? Kubwanyuka: Kuphwanyika. Chitsanzo: Chimene anaumba chabwanyuka. Kubwanyula: Kumenya. 102