Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 102

Paphata pa Chichewa Kubodetsa: Kupusitsa. Chitsanzo: Mukapusa akubodetsani. Kubodetsana: Kupusitsana. Chitsanzo: (1) Anthuwatu akungobodetsana. (2) Ukapanda kuchenjera akubodetsanso. Kubolobosha: (a) Kuchita zinthu mosalongosoka. Chitsanzo: (1) Akakhala kuti sakufuna amangoboloboshabolobosha n’kuzisiya. (2) Sindinawerenge bwino, ndangobolobosha. (b) Kulemba zinthu zosaoneka bwino. Chitsanzo: Mwanayu amangobolobosha akamalemba. Kubooka: Kupezeka mosavuta. Amatanthauzanso kukha- la ndi penapake pamene pali boo kapena pamene pakhoza kutulukira zinthu. Chitsanzo: Koma ndiye mango abookatu! Kuboola m’makutu: Kusokosera. Chitsanzo: Iwe usatiboole m’makutu! Zikapangira uko phokoso lakolo! Kuboola m’mimba: Kukuopseza, kupangitsa wina kuti asowe mtendere. Chitsanzo: Akuchita zimenezi kuti angondiboola m’mimba. Kuboola mtambo: Kupita dziko lina pandege. Chitsanzo: Chaka chino ndiboola mtambo. Kubooleza: Kunena zenizenizo. Chitsanzo: (1) Atandifunsa za nkhaniyo ndinangobooleza. (2) Tangoboolezani, anakuuzani chiyani? 101