Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 101

Paphata pa Chichewa Chitsanzo: Nyimbo imeneyi imandibanda. Kubandulana: Kumenyana. Chitsanzo: Ana amadererana ajatu abandulana lero. Kubaya mumtima: Kupweteka mumtima. Chitsanzo: Zimene anena zandibaya mumtima. Kubaya suti: Kuvala suti. Chitsanzo: Adutsa pompa atabaya suti yawo. Kubenthulako: (a) Kunenako pang’ono. Chitsanzo: Bwerani ndikubenthulireni zimene ananena. (b) Kuswa, kugamphula chinthu. Chitsanzo: Ndani wabenthula khaka langa? Kubereka kopenyetsa kamtengo: Kubereka kwambiri. Chitsanzo: Anthu akuberekana kwambiri m’dzikoli, moti kuberekana kwake ndi kopenyetsa kamtengo. Nanga dziko ling’onong’onoli! Kubetcha: Kupereka chinachake monga chitsimikizo choti zimene ukunenazo zichitikadi. Chitsanzo: Anthu onse abetcha ndalama ndipo akuti timu imeneyi ipambana. Kubetsa: Kuluza, kusaganiza bwino, kutaya. Chitsanzo: (1) Kukwatira ndi amene uja ndi kubetsa. (2) Koma ndiye mwabetsatu, kugulitsa nsalu 100 kwacha! Kubinya: Kuvulala pamalo olumikizira mafupa. Chitsanzo: Akuyenda pintchapintcha chifukwa wabinya. Kubisala pachipande: Kunama. Chitsanzo: Mwabisalatu pachipande, nsana ukuonekera. 100