Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 10

Paphata pa Chichewa Ana akumpanda: Ana a mabwana, ana okula moyo wofewa. Chitsanzo: Usadzayerekeze kufunsira mwana wakumpanda. Ana akumpani: Mbewa. Chitsanzo: Munthu wamtundu wanji wobadwira ku Mala- wi kuno koma osadziwa ana a kumpani! Ana ndi chuma: Mawuwa amatanthauza kuti tsogolo la dziko limadalira ana. Chitsanzo: Anthu ambiri anayamba kubereka ana ochuluka poganiza kuti ana ndi chuma. Ana ofewa: Ana onjoya, osangalala ndi moyo. Chitsanzo: Ife ndi ana ofewa, sitidandaula ndi zambiri. Anabwereketsa makutu: Ndi wosamva. Chitsanzo: Achimwene anuwa anabwereketsa makutu. Anafa mutu: (a) Saganiza. Chitsanzo: Anzanuwa anafa mutu, sangakuthandizeni mutawafunsa maganizo. (b) Kutengeka ndi mnyamata kapena mtsikana mpaka kufika posokonezeka. Chitsanzo: Zimene umachita zija zimasonyeza kuti unafa naye mutu mtsikana uja. Anagonerapo onsewa: Mawuwa amanenedwa posonyeza kuti munthu wina ankangokhulupirira aliyense, anakhulupirirapo onsewa. Chitsanzo: Mnyamata uyu anagonerapo onsewa. 9