Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale | Page 66

Ngale wo n’kumawuza anthu kuti Kino ndi mkazi wake akubwera. Anthu awiriwa anatulukira munsewu wakale uja ali ndi chisoni chachikulu. Nthawi zonse Kino ankayenda kutsogolo ndipo mkazi wake ankamutsatira pambuyo. Koma ulendo uno, Juana ankayenda pambali pake. Dzuwa linali likutsetsereka kumbuyo kwawo n’kumapita kuka- lowa. Izi zinachititsa kuti zithunzithunzi zawo zitamukire kutsogolo. Ki- no anali atakolekera mfuti paphewa. Juana anali atanyamula chinachake munsalu ndipo chinthucho chinali magazi okhawokha. Maso ake anali atatupa ndi kulira. Nayenso Kino misozi inkangotsikira m’mimba, paja amuna kulira kumawavuta. Anthu amanena kuti Kino ankawoneka wamantha kwambiri. Ena amati ankawoneka mowopsa ngati mkango. Zinali zowonekeratu kuti moyo wa anthu awiriwa unali utasinthiratu. Pamene ankayenda, anthu owamvera chisoni ankawachingamira ndi maso ndipo amene anayima panjira ankawapisa kuti adutse. Palibe ame- ne anawayankhula. Kino ndi Juana anayenda maso ali patsogolo. Sanayang’ane kumanja kapena kumanzere mpaka anakafika m’mudzi wakwawo. Nawonso an- thu a nyumba zapafupi anawalandira ndi maso ndipo Juan Tomas ana- pita kwa m’bale wakeyo kuti akamugwire chanza, koma dzanja lake li- nabwerera m’malere. Imeneyi inali nthawi yolakwika kwambiri kupe- reka moni. Kino ndi Juana anadutsa panali phulusa la nyumba yawo ija ndipo sanayang’anepo n’komwe. Anayenda n’kudutsa tchire linali pafupi ndi doko, malo omwe Kino anapherapo wachifwamba uja. Kenako anakafi- ka kudoko ndipo kumeneko anachita zinthu modziletsa kwambiri moti sanayang’ane bwato lawo lobowoka lija ngakhale pang’ono. Anthu anawona Kino akuchotsa mfuti anakolekera paphewa ija, ke- nako anayisiya pansi. Kenako anatulutsa ngale yamtengo wapatali ija kuchokera m’malaya ake. Anayiyang’ana kwa kanthawi ndipo anawona maso a anthu a mtima wachikolopa, omwe ankafuna kumubera. Ana- wona nyumba yake ikupsa mpaka pansi. Anawonanso anthu atatu om- we anawapha kuphiri kuja. Misozi inalengeza m’maso mwake atawona mwana wake Coyotito, yemwe anaphwasulidwa mutu ndi chipolopolo chankhanza. Mtima wake unayamba kumuwawa kwambiri moti ngale- 60