Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale | Page 65

Ngale mveka ngati mwana zikamalira.” Mtima wa Kino unali utasungunukiratu ndi mantha. Ankadziwa kuti amene akulirayo ndi mwana wake Coyotito. Kunena zowona, tsoka likalimba umakuwotcha ndi mkute wadzana. Coyotito uja analiranso ndipo munthu anali ndi mfuti uja anazindikira pemene kulirako kunkachokera. Munthu ameneyu sanali woti akalozetsa mfuti yake n’kuphonya. “Mwinadi ndi nyama, ndikuganiza kuti itseka pakamwa pake ndi chipolopolo ichi,” anatero akutukula mfuti ija ndipo posakhalitsa pan- amveka chiphokoso choswa makutu kuti pho-o-o-o, ndipo kulira kuja kunaleka. Kino anachita zilope n’kulumphira munthu anawomba mfutiyo mpeni uli m’manja. Posakhalita mpeni wakewo unagwira ntchito yake ndipo unalowa mopanda kudziletsa pakhosi pa munthuyo. Pamene ankazula mpeniwo, anawuyendetsa mwamphulupulu n’kuzinga winan- so amene anagona pansi paja ndipo dzanja linali anali akutola mfuti ija. Apo ndiye Kino anaterera ngati mlamba. Amene anatsala uja anadzam- batuka asakudziwa kuti chikuchitika n’chiyani ndipo analumphira padziwe lija n’kusambira mpaka kuwoloka. Posakhalitsa anayamba kukwera mwala wina kuti athawe, koma anachedwa. Ndi kuwala kwa mwezi uja Kino ankatha kumuwona bwinobwino moti anatukula mfuti ija n’kuwomba, koma anaphonya. Chifukwa cha phokoso la mfutiyo, munthu uja anatsetsereka pamwalawo n’kugweranso m’madzi. Kino anamutsatira ndipo atamuyandikira, anatukulanso mfuti ija n’kupanga una pakati pa maso ake. Kino ankatha kumva kuti chinachake chalakwika chifukwa mdani wake uja atangolekana nawo moyo wapadziko lapansi, anamva mkazi wake akulira m’phanga anabisala muja. Kulira kumeneku kunali kwachilendo kwambiri m’makutu mwake. ♦ Aliyense ku La Paz amakumbukirabe za kubwerera kwa banjali. Zimamveka kuti anatulukira chakumadzulo. Anthu atangowawona anayamba kuwatsatira ndipo ana ogulugusha anathamangira m’makwa- 59