Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale | Page 62

Ngale hatchi uja nayenso ankayenda wa Adamu chifukwa kumaloku sikunali koti n’kufika hatchi. Atangofika padziweli, anthu awiri ankatsogola aja anayenda mozungulirazungulira padziwelo kuti atsimikitse kuti palibe munthu. Sipanatenge nthawi kuti azindikire zoti pamalowo panali anthu. Sanakayikire zoti Kino ndi mkazi wake adutsa kudzera pamwala unali ndi zomwera zowandikawandika uja. M’modzi wa iwo anakwera mwalawo n’kuponya maso ake chakutsogolo koma sanawone munthu. Kenako anatsika n’kuyamba kukonkha kukhosi kwake ndi madzi a padziwe lija. Munthu anali ndi mfuti uja anabzala matako ake pansi n’kumapuma. Nayenso anali atatheratu ngati chikabudula cholimira. Anzake aja anakhala pambali pake n’kumasuta fodya. Kino anangoti maso ga pamene anthuwo anakhala moti posakhalitsa anawawona aku- dya chakudya chawo. Kenako mdima wowopsa unagwa mphirimo ndipo Kino anamva mawu chapansipansi. Anali Juana ndipo ankatonthoza Coyotito kuti asasokosere kwambiri. Kino sanasiye kuyang’ana anthuwo moti anazindikira kuti awiri agona. Koma m’modzi ankayang’anira anzakewo mfuti ili m’manja. Kenako Kino anapita kukalowa m’phanga lomwe munali Juana. “Juana, ndapeza njira,” anatero Kino. “Komatu akhoza kukuphani.” “Ndikangopeza njira yolandira mfuti ili ndi munthu m’modziyo ndiye kuti ndawatha,” anatero Kino. “Sindikukayikira kuti ndikhoza kuthana naye chifukwa awiri akugona.” Juana anagwira nkono wa mwamuna wakeyo. “Komatu akhoza kuwona zovala zanu zoyerazi ndi kuwala kwa nyenyeziku.” “Usadandawule ndi zimenezo,” anatero Kino. “Ndikungofunika ndingotsika mwezi usanatuluke. Ndikangotenga mfutiyo andimva madzi.” Kino ankadziwa kuti kameneka kakhoza kukhala komaliza kuwonana ndi Juana. Choncho anasakasaka mawu abwino m’mutu mwake ndipo atawapeza anati: “Ndimakukonda kwambiri mkazi 56