Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale | Page 60

Ngale Kino ndi mkazi wakeyu ankapita chakum’mwera n’kukasiya madindo a mapazi, kenako n’kuloweranso chakumapiri kuja n’kumakayenda pamiyala. Anayenda mpaka miyendo kulowa m’mimba. Tsopano dzuwa linali litayamba kulowa. Pofuna kupeza malo ogona, Kino anakwera mwala wina ndipo chakuseri kwa mwalawo anawona malo ena obiriwira ndi zomera. Pa nthawiyi madzi anali m’botolo aja anali atatha, choncho ankafunikira madzi ena. Kino anaponya maso pamene panali zomerazo ndipo anawona dziwe lamadzi. Posakhalitsa anakoka mkazi wakeyo mpaka kufika pamwamba ndipo anayamba kuyenda motsata mwalawo mpaka anakafika kumene kunali zomera zija. Pamene Kino ndi Juana ankayenda motsatira mwalawo, ankatha kuwona dera lonse mpaka kukafika kunyanja. Kenako anatsika pamwalawo n’kufika padziwe lija. Zikuwoneka kuti madzi a padziweli ankatuluka pakati pa mwala wina. Madziwa ankayenda n’kumagwera kuchiphedi china. Akagwera kumeneko ankangozimiririka osawonekanso. Chifukwa cha madziwa, pamalowa pankabwera nyama zosiyanasiyana. Zina zinkayenda mtunda wawutali zedi kuti zidzafike kumeneku. Nazonso nyama zolusa sizinkasowa pa- malowa moti nyama zing’onozing’ono zikapusa, zinkajiwa n’kunenepetsa zinzawozo. Juana anali atatheratu ndi kutopa moti anangofikira kukhala pansi n’kuyamba kusukusulitsa Coyotito yemwe anali thukuta lokhalokha. Anatungiranso madzi m’botolo lija n’kumupatsa kuti amwe. Kino anali ndi ludzu kwambiri moti anawerama padziwelo n’kuyamba kumwa madzi ngati ngamila. Atamaliza anakhala pansi n’kumayang’ana Juana akuyamwitsa Coyotito. Mphamvu zitabwerera, anadzuka n’kupita kukasuzumira kumene ankachokera kuja. Koma ikakuwona litsiro si- kata. Kino anawona anthu atatu aja akubwera chapatali. Juana anatembenuka n’kuyang’ana mwamuna wake ndipo anawona mantha amene analembeka pachipumi chake chosendeka chija. “Bwanji bambo a Coyo?” anafunsa Juana. “Anthu aja akubwera kuno! Ndikuganiza kuti posachedwapa afika 54