Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale | Page 59

Ngale mwala chija ndipo Juana anawona mwamuna wakeyo akumuyangana miyendo yake yomwe inali italembekalembeka ndi minga komanso udzu. Nawonso mapazi ake anali atachekekachekeka ndi miyala yakuth- wa. Powopa kumutayitsa mtima mwamuna wakeyo, Juana anaphimba miyendoyo ndi siketi. Kenako anapereka botolo lamadzi lija kwa Kino kuti aphe ludzu, koma Kino anakana. Chimenechi ndi chimene chinali chochititsa chidwi ndi Juana. Ngakhale zinthu zithine bwanji, sankayi- wala kuyika patsogolo zofuna za banja lake. Iye akanalolera kukhala ndi ludzu, bola banja lake lonse limwe madzi. Komabe, kuthamanga ndi mwana pansana kunja kukuwotcha kwambiri kunachititsa kuti thupi lake lifowokeretu. Ngakhale ankafuna kubisa zimenezi, Kino anazindikira. “Juana,” anatero Kino, “Ineyo ndipitirizabe kuthawa, iweyo ubisale. Anthuwa akufuna ineyo moti sindikukayikira kuti anditsatira m’mapiri- wa. Chimene ndikufuna kuchita ndi choti, ndiwakope kuti anditsatire kumapiri. Ukangozindikira kuti adutsa, iweyo ubwerere n’kuthawira ku Loreto kapena ku Santa Rosalia. Ngati nditakwanitsa kuwazemba, ndi- dzabwera kudzakufunafuna. Iweyo watopa kwambiri moti ndikuwona kuti sikukhala kukuganizira ngati nditakuwuza kuti upitirizebe kukwera chitundachi mwana ali kumbuyo. Imeneyi ndi njira yokhayo imene ndingapulumutsireni.” Juana anayang’ana mwamuna wakeyo momumvera chisoni. “Ayi,” anatero. “Tiyeni tithawire limodzi.” “Ineyo ndikhoza kupita patali kwambiri ngati nditakhala ndekha,” anatero Kino. “Uyikatu moyo wa mwanayu pangozi ngati utapitiriza kunditsatira.” “Ayi,” anatero Juana. Kino anayang’ana nkhope ya mkazi wakeyo kuti awone zizindikiro za mantha, koma sanaziwone. Maso ake anali ngwe-e. Iye anali atalimba mtima moti anapitirizabe kuyenda. Posakhalitsa anayamba kuyenda pamiyala. Kino ankadziwa kuti owasakasaka aja sangafike kumeneku. Zikanawatengera nthawi yayitali kuti azindikire zoti kumeneko kwadutsa anthu. Pofuna kuwapusitsa, 53