Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale | Page 58

Ngale “Anthu ena akutifunafuna,” anatero Kino, “Tiye tithawe mofulumi- ra!” Mphamvu zinali zitamuthera ndipo nkhope yake inali itagweratu. “Mwinatu ndingodzipereka kuti iweyo ndi mwanayu akusiyeni. Sindikukayikira kuti akangozindikira kuti tabisala pano atipha.” Nthawi yomweyo Juana anathamanga n’kukagwira mapazi a Kino. “Musayerekeze kuchita zimenezo chonde, ndagwira mwendo wanu!” anatero Juana. “Mukuganiza kuti angakusiyeni wamoyo ndi ngale muli nayoyo?” Kino anayendetsa dzanja lake n’kupisa pamene anasunga ngale ija. “Komatu palibe chimene tingachite kuti atisiye,” anatero motaya mtima. “Koma musapite chonde,” anachonderera Juana. “Akakuphani ineyo ndilowera kuti ndi mwanayu?” Kino sanasunthe. Zinkawoneka kuti zimene ankanena mkazi wakeyo zayamba kulowerera m’mutu mwake. Kenako Juana anati: “Mukuganiza angandisiye wamoyo ineyo? Nanga mwana wathuyu, mukuganiza kuti angangomusiya?” Mawu a mkazi wakewa anamusintha. Maso ake anasinthanso n’ku- mawoneka ngati a chimbalangondo. “Basi tiye,” anatero Kino. “Tiye tithawire kumapiri. Mwina sangatipeze ngati titathawira kumapiri.” Kino anatola kachikwama kake n’kulunjika kumapiri omwe anali chakum’mawa. Chifukwa cha mantha, Kino ndi mkazi wakeyu ankatha- manga paliwiro lowopsa pakati pa mitengo yaminga komanso tchire. Iwo analibenso nthawi yoganizira zofufuta mapazi omwe ankasiya m’mbuyo. Kino ankafuna kuthawira kumapiri ngati mmene nyama zam- biri zimachitira zikamasakidwa. Posakhalitsa anayamba kuthamanga pamiyala. Chifukwa cha kuten- tha, onse anali thukuta kamukamu ndipo mwawefuwefu anayamba kukwera chitunda. Tsopano anali atatalikirana ndi anthu aja moti anayamba kuyenda modekha. Kino anakwera chimwala chachikulu n’kuyang’ana patali ngati anthu aja ankawatsatira, koma sanawone ali- yense. Juana anakhala pamthunzi wamwala wina ndipo anatulutsa boto- lo la madzi n’kumupatsa Coyotito. Posakhalitsa Kino anatsika pachi - 52