Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale | Page 57

Ngale wake kuja. Iye ankadziwa kuti anthuwo sangalephere kuzindikira kuti pamalowo pali anthu, makamakanso akawona kuti wina amayesa kufufuta mapazi ake ndi nthambi yamtengo. Anthuwa sanali oti unga- wapusitse. Choncho Kino ankafuna kuti anthuwo akangofika pamene ankafufuta mapazi paja, awawukire. Iye ankalakalaka atalumphira munthu anali pahatchi uja. Ankadziwa kuti kusokoneza ameneyu kungachititse kuti enawo akhale opanda mphamvu. Cholinga chake chi- nali kulanda mfuti n’kuyigwiritsa ntchito polanga enawo. Pamene anthuwo ankayandikira, Kino anakonzekera kuti awajowere. Posakhalitsa Juana anamva kulira kwa hatchi. Pa nthawi imeneyi Coyotito anali akuchita phokoso chapansipansi. Mwansanga, Juana ana- munyamula mwana wakeyo n’kumutseka pakamwa. Ofufuza mapazi aja atayandikira, Kino ankangowona mapazi a anthu awiri aja komanso a hatchi ija. Anthuwa anavala nsapato zakutha komanso mabuluku othimbirira. Kenako Hatchi ija inayima n’kuyamba kuyendetsa mutu wake kwinaku ikulira. Nthawi yomweyo ofufuza mapaziwo anatembenuka n’kuyang’anitsitsa makutu a hatchiyo kuti awone ngati yazindikira kuti penapake pabisala anthu. M’mimba mwa Kino munabwadamuka ndi mantha. Kwa nthawi yayitali anthuwo ankangoyang’ana munsewu muja koma sanawone chizindikiro chogwira mtima chamapazi a anthu. Kenako anapitiriza ulendo wawo akuyang’ana mosamala munsewumo. Munthu anali pa- hatchi uja anapitirizabe kuyenda pambuyo pawo. Mtima wa Kino una- khalako pansi. Komabe, ankadziwa kuti mavuto akadalipo. Sankaka- yikira kuti anthuwo akhoza kubwereranso. Anthu aja atangotha kamtunda pang’ono, Kino anadzambatuka n’kulowera kumene kunali mkazi wake. Ulendo uno sanavutike ndi kufufuta mapazi ake. Ankadziwa kuti pali kale zizindikiro zambirimbiri zimene zingawagwiritse. Timitengo tambirimbiri tinali titathyoledwa ndi mapazi awo, ndipo timiyala tina tinali titasuntha chifukwa chaku- lemera kwa matupi awo. Kino anayamba kuchita mantha kwambiri. Ankadziwiratu kuti akhoza kugwidwa. Posakhalitsa anafika pamene panali Juana akuchita befu ndipo mkazi wakeyo ankangomuyang’ana ndi nkhope yamafunso. 51