Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale | Page 56

Ngale mutu basi. “Bwanji?” anafunsa Juana. “Takhala chete,” anatero Kino atakweza dzanja lake. “Mumabwebwetatu inu.” “Ndimabwebweta?” Koma Kino analephera kukhazikika chifukwa cha mantha. Anayang’ana pamene ankasunga mpeni wake n’kuwutulut- sa ndipo Coyotito anali akungoseka pamene anamukhazika paja. Ke- nako Kino anati, “Mwanayu asamalongolole atigwiritsa.” Anamvetseranso mwatcheru, ndipo khutu lake linatola phokoso lina lomwe linamuthandiza kudziwa kuti kukubwera chinachake. Nthawi yomweyo anadzuka n’kuyenda mozemberera kulowera chakunsewu ku- ja. Atayandikira nsewuwo anabisala kuseri kwa mtengo wina n’kumam- waza maso ake. Kino anawona anthu atatu akubwera. M’modzi anakwera hatchi ndipo awiri ankayenda wapansi. Kino atangowona zimene ankachita anadziwiratu kuti anthuwo akusakasaka iwowo ndipo mantha anamug- wira. Anthu awiri ankayenda wapansi ndipo ankawonekeratu kuti aku- fufuza madindo a mapazi. Anthuwa anali anamatetule chifukwa anka- tha kuzindikira malo amene padutsa munthu pongowona udzu, timiten- go komanso mmene mchenga ulili. Akangowona chizindikiro chili- chonse choti phazi la munthu linadiliza penapake, ankalondola zizindikirozo mpaka kukafika kumene wapita. Munthu amene anakwera pahatchi uja ankayenda pambuyo pa anthu awiriwa ndipo munthuyu ananyamula mfuti. Anthu awiri ankayenda wapansi aja ankasakasaka Kino ndi mkazi wake ngati mmene alenje amasakira nyama. Koma wapahatchi uja ankangodikira kuti anthuwo apezeke ndiyeno awalawitse chipolopolo. Munthu ameneyu sanali wamasewera chifukwa akawomba mfuti, chipo- lopolo chake sichinkapita pachabe. Anthu awiri ankayenda wapansi aja anayamba kupanga phokoso ngati agalu achiwewe. Zinkangokhala ngati amva fungo lanyama. Ata- ngomva phokosolo, Kino anatulutsa mpeni wake. Iye anayamba kuga- nizira zomwe angachite anthuwo akayamba kulowera kunali mkazi 50