Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale | Page 48

Ngale munthu woti amuyimbire mtiwiso n’kumuwuza kuti masiku akale aja sadzabwereranso. Thupi la munthu wosadziwikayo komanso mpeni wamagaziwo zinalanduliratu kuti moyo wawo sudzabwereranso mwa- kale. Iye anazindikira kuti chomwe akufunika kuchita tsopano ndi kupu- lumutsa banja lake. Zowopsa zimene anawonazi zinachititsa kuti ululu ankamva patsaya komanso pamwendo wake uja ubalalikiretu. Mofulumira anag- wira miyendo ya munthu wakufayo n’kuyamba kumukokera patchire. Atachoka kumeneko anapita pamene panali Kino n’kukayamba ku- mupukuta chipumi chake chatsoka chija, chomwe chinawumbudzid- wanso mwankhanza. Juana anapukuta magazi omwe ankatuluka pachi- pumipo ndi siketi yake. “Basitu atenga ngale ija. Ngale ija yapita Juana,” anatero Kino modandawula. “Usadandawule mwamuna wanga. Palibe amene watenga ngale yathu. Ili ndi ineyo. Ndayipeza pansi pa mwala m’mbali mwa njirayi. Koma mukumva zimene ndikunenazi? Ngale yathu sinatengedwe,” ke- nako anayang’ana mpeni uja n’kunena kuti, “Koma tawonani mwapha munthu! Tiyeni tithawe mwansanga anthu angatigwire n’kutipha. Tiyeni tithawe dzuwa lisanatuluke.” “Komatu anachita kundiwukira. Nanga ine ndachita kukamupeza pakhomo pake ngati?” anatero Kino. “Ndamupha podziteteza.” “Mwakumbukira zimene zinachitika dzulo zija?” anafunsa Juana. “Mukuganiza kuti pali amene angamvetsere zimenezo? Mwakumbukira zimene ogula ngale aja anachita? Mukuganiza kuti zingakhale zomveka titawawuza zimenezi ndi chakukhosi chimene akutisungira chifukwa chowakaniza kuwagulitsa ngaleyi?” “Sizingamvekedi,” anatero Kino. “Ukunena zowona Juana.” Mtima wake unali utalimbanso tsopano. Iye anali atasandukanso munthu wam- wamuna. “Pita kunyumba ukatenge mwana,” anatero Kino. “Ukatengenso ufa wonse womwe tili nawo. Ineyo ndithamange ndikayambe kukankha bwato lathu. Chita machawi, undipeza kudoko.” 42