Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale | Page 46

Ngale Gawo 5 Usiku umenewo Kino anamva chinachake chikuyenda pafupi ndi pame- ne anagona moti anatsegula maso ake. Iye sanasunthe ngakhale pang’ono. Ndi maso ake okha amene ankayendayenda n’kumazungulira m’nyumbamo kuti awone kuti n’chiyani. Mothandizidwa kachizirezire ka mwezi, Kino anawona Juana akuyenda molowera kumene ankakole- za moto kuja. Iye anangomva kaphokoso kakang’ono pamene Juana an- kasuntha fuwa lina. Kenako anayamba kuyenda molowera kukhomo. Mwatsoka lanji, Kino anazindikira zomwe mkazi wakeyo ankafuna kuchita moti anadzuka n’kuyamba kumutsatira atakwiya kwambiri. Iye ankatha kumva mtswatswa wa mkazi wakeyo akuyenda molowera ku- doko. Posakhalitsa anayamba kuwona momwe mapazi ake ankapaza. Poganiza kuti palibe amene akumutsatira, Juana anayamba kuyenda pang’onopang’ono powopa kuterereka ndi timiyala ta mukanjirako n’kugwa. Pa nthawiyi mpamene anamva mdidi ndipo atatembenuka an- awona mwamuna wake akumutsatira. Juana anachita tsembwe ndipo pochita mantha kuti amulanda ngale anatenga pansi pa fuwa lija, anan- yamula dzanja lake kuti ayitaye koma munali m’mbuyo mwa alendo. Ki- no anamuwaza mbama lowonetsa chizungulire moti linamunyamula n’kumugwetsera pansi. Kino anayamba kuyang’ana mkazi wakeyo mokwiya kwambiri. Misozi inayamba kutsika m’masaya mwa Juana. Zimene zinachitikazi zi- namutsimikizira Juana kuti Kino akhoza kupha munthu. Kino anatola ngale ija n’kumalowera kudoko. Zikuwoneka kuti nayenso anali asa- nayambe kuganiza bwinobwino chifukwa cha nkwiyo. Atayenda kamtunda pang’ono, Kino anamva phokoso lodabwitsa patchire lapafupi. Pamene ankatulutsa mpeni wake, anangozindikira wayamba kuwona nyenyezi. Munthu wosadziwika ndi amene ana- mumenya ndipo m’maso mwake munali mutachita mdima. Posakha- litsa, manja adyera anayamba kumufufuza m’matumba. Koma munthu- yu akanadziwa sakanachita zimenezo. Chidwi chake chonse chili pofufuza m’matumbamo, Kino anaphiriphitha n’kumubaya ndi mpeni. Mpeniwo unalowa wonse ndi chikumbu chomwe. Zikuwoneka kuti ka- modzi kokhaka kanali kokwanira chifukwa munthuyo anamusiya 40