Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale | Page 42

Ngale yakoyi. Ukanangovomera ngakhale amakubera. Apatu wangokhala nga- ti ukutsutsana ndi zimene makolo athu akhala akuchita. Ndayamba ku- chita mantha kuti chinachake chikhoza kukuchitikira.” “Ine sindikuchita mantha. Ndichita mantha ndi chiyani?” anafunsa Kino. “Anthu andiwopseze chifukwa cha ngale yangayi? Ayi, sindilola kuti wina anditengere kumtoso ngati maliro a njoka. Amene atalimbane ndi ine adziwanso!” “Ndangofuna ndikuwuze monga m’bale wanga,” anatero Juan To- mas. “Koma n’kutheka kuti ukulondola. N’kuthekanso kuti ngale yakoyi ukhoza kukayigulitsa ndalama zochuluka kumene ukunenako. Koma kodi wakonzeka kukwera mapiri omwe ungakumane nawo kuti zimene- zo zitheke?” “Ukutanthawuza chiyani?” “Ndikungowopa kuti chinachake chikhoza kukuchitikira. Panopa ukungokhala ngati ukuyenda njira yachilendo ndipo kumene ukupita sukukudziwa.” “Koma nanenso ndikuwuze Juan Tomas. Munthune ndavutika mokwanira ndipo sindilola chilichonse kundilanda mwayi umene nda- pezawu. Ndinyamuka masiku akubwerawa kupita kukagulitsa ngale yangayi patsidya lanyanja,” anatero Kino. “Inde, ukuyeneradi kupita,” anavomereza Juan Tomas. “Koma ndikuganiza kuti kumene ukupitako sikukachitika zosiyana ndi zimene zachitika kunozi. Bolanso kunoko kuti uli ndi anzako komanso ineyo, mchimwene wako. Kumene ukupitako, ngakhale mphemvu kapena utit- ili sizikukudziwa.” “Nanga ndiye mukufuna nditani?” Kino anayankhula mowawidwa mtima. “Sindikufuna kuti mwana wangayu adzafe ali mphawi. Ndikufuna azidzasangalala. Koma zikuwoneka kuti pali ambiri omwe satifunira zabwino. Amasangalala akamatiwona tikuvutika. Koma ayi, ndimenya nkhondoyi mpaka pamapeto. Anzanga anditeteza.” “Akhozadi kukuteteza. Koma angakuteteze ngati miyoyo yawo sili pachiwopsezo,” anatero Juan Tomas. Kenako anayimirira akunena kuti, “Koma ndikufunira zabwino zonse. Mulungu akhale nawe m’bale 36