Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale | Page 39

Ngale ladyera la wogula uja silinachoke pangaleyo. Posakhalitsa, panja paja panamveka anthu akupereka njira kwa ogula ngale atatu anapita kukayitanidwa aja. Khamu la anthulo lin- acheteka kaye. Palibe ankadzikanda kapena kutsokomola powopa kuti phokoso lake lingachititse kuti zina zimene zingakambidwe mu ofesi muja ziwadutse. Pamene anthuwo ankalowa, Kino anangokhala chete. Iye ankangochita chidwi ndi nkhope zawo. Pa nthawiyi Kino anamva kukodola kumbuyo kwake ndipo atatembenuka anawona mkazi wake Juana. Pamene ankatembenukanso, anali atalimba mtima. Anthu atatuwo asanayang’ane ngale ija, munthu wonenepa uja ananena kuti: “Achikulirewa abwera kudzagulitsa ngale yawo ndiye ndawawuza mtengo wongobetsa wa chinthu chili apachi. Koma zik- uwoneka kuti sakugwirizana nazo. Tachiwonani mosamala anzanganu, ndiyeno mundiwuze mtengo umene mungachigule.” Kenako anatem- benukira kwa Kino. “Uwonetu eti, nanga ndawawuza mtengo ngati? Uwone wekha zimene atanene.“ Amene anayamba kutsirira ndemanga anali wogula wina yemwe anali wowonda zedi. Munthu ameneyu anadzidzimuka atawona ngaleyo. Ndiyeno anayitola n’kuyamba kuyiyang’ana mwachidwi. Koma kenako anayiponyeranso patebulo paja ngati nyansi. “Ine sindingagule ngale imeneyi,” anatero. “Kugula chinthu chimen- echi n’kuwononga ndalama!” Kenako wogula wachiwiri pa atatuwo, yemwe anali wachinyamata komanso wowoneka watimanyazi tabodza, anawerama n’kutola ngaleyo kwinaku akuyiyang’ana mwachidwi. Koma posakhalitsa anayamba kuseka chapansipansi. “Ngaleyi ndi yofewa kwambiri,” anatero munthuyo. “Singachedwe kuchoka mtundu ndipo ikhoza kufwifwiratu pakangotha miyezi yochepa.” Nayenso wachitatu anatenga ngaleyo n’kumayiyang’ana. “Ndili ndi kasitomala wina yemwe amakonda ngale zazikulu chonchi,” anatero. “Ndikhoza kukugula ngaleyi pamtengo wa 500 pesos, ndipo ineyo ndingakayigulitse kwa munthuyo pamtengo wongotaya wa 600 pesos.” 33