Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale | Page 35

Ngale pambuyo ngati ngolo, kunsana kwake atabereka Coyotito. Kenako analunjika nsewu wopita m’tawuni ndipo anthu a nyumba zapafupi aja anawatsata mwawunyinji. Ndiye popeza tsikuli linali lofunika zedi, pambali pa Kino panali mchimwene wake, Juan Tomas. “Usakachitetu zogona anthu ake ndi akuba. Zingakhale zomvetsa chisoni kwambiri ngati atakakunenerera mpaka kukugula pamtengo wolira,” anatero Juan Tomas. “Zowonadi, anthu amenewa ndi amambala kwabasi,” anavomereza Kino. “Sitikudziwa kuti m’madera ena anthu amagulitsa ngale pamitengo yotani,” anatero Juan Tomas. “Nanga tingadziwe bwanji ngati ogula ngale akunowa amatigula pamitengo yabwino? Ndimalakalaka tsiku lina nditazadziwa mitengo yomwe amawagula kumene amakagulitsako akatigula ifeyo kunoko.” “Zowonadi,” anatero Kino, “koma nanga tingadziwe bwanji ngati pali amene anayamba wachokapo kuno n’kupita m’matawuni ena?” Pamene ankayenda, khamu la anthu linkawatsatira lija linkangokuli- rakulira. Atawona khamuli, Juan Tomas anayamba kuchita mantha ndipo anati: “Iweyo usanabadwe Kino,” anayamba motero Juan Tomas, “akuluwakulu amtundu wathu anapeza njira yoti azigulitsa ngale zawo pamitengo yabwino. Anaganiza zopeza munthu woti atenge ngale zonse n’kukazigulitsa kumzinda wawukulu.” “Ndinamvadi zimenezo,” anatero Kino. “Ndimawona kuti analinga- lira bwino kwambiri.” “Posakhalitsa anapezadi munthu n’kumupatsa ngale zawozo,” anapitiriza Juan Tomas, “Koma munthuyo atangochoka kuno, sanabw- ererenso. Kungochokera tsiku limenelo palibe anamvanso za iye. Zimamveka kuti achifwamba ndi amene anamupotokola khosi n’kutenga ngale zonse. Patapita nthawi anatumizanso wina, ndipo atan- gochoka kuno, nayenso sanawonekenso. Atawona kuti njirayi itha anthu, anangoganiza zobwerera ku njira yakale ija.” 29