Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale | Page 34

Ngale Gawo 4 M’mawa watsikuli, mbiri inamveka yoti Kino akagulitsa ngale yake m’tawuni ya La Paz. Anthu onse a nyumba zoyandikira anamva za nkhaniyi. Nawonso ogulitsa m’mashopu a m’tawuniyi sinawaphonye. Nkhaniyi inafikanso kutchalitchi kuja. Koma koposa onsewa, inakafikan- so kwa anthu ogula ngale omwe anakhala m’mawofesi awo n’ku- madikirira mphuno zili m’mwamba. Dzuwa linalawira kuwomba m’mawa umenewo. Mabwato ankan- goti ndengundengu m’mbali mwa nyanja. Zikuwoneka kuti pa tsikuli palibe nsodzi ndi m’modzi yemwe amene anaganiza zolowa panyanja kuti akafufuze ngale. Limeneli linali tsiku lapadera kwambiri kwa Kino ndi mkazi wake. Chisangalalo chawo chinkafanana ndi chimene anali nacho Coyotito atangobadwa. M’mawawu, Juana anaveka mwana wake zovala zimene ankazidalira. Kenako anamanga tsitsi lake ndi chingwe chofiyira n’kuva- la siketi yomwe ankayivala pazochitika zapadera. Pamene dzuwa linka- yamba kukwera, banjali linanyamuka. Kino anali atavala zovala zake zoyera, zomwe zinali zachikale komanso zofwifwa. Iye sankakayikira kuti limeneli likhala tsiku lomaliza kuzivala. Mawa, mwinanso titi mad- zulo a tsikuli, akanakwanitsa kugula zovala zatsopano. Anthu oyandikana nawo nyumba aja ankangoyang’ana pakhomo pa Kino ali m’nyumba zawo. Nawonso anali atatchenatchena n’kumadikiri- ra kuti awuyambe. Iwo anali atagwirizana kuti limeneli ndi tsiku lapadera kwambiri kwa asodzi onse. Nawonso ankawona kuti angachite bwino kupita nawo kuti akawonerere mnzawo wakuntchito akugulitsa ngale yake. Juana ananyamula Coyotito kuti nayenso akawone chilichonse chomwe chikachitike. Kino anavala chisoti chake chakhonde komanso nsapato zake zotopa n’kubowoledwa ndi chisongole. Ngale yamtengo wapatali ija anali atayikutira mukansanza kofewa. Kansanzako anakayi- ka m’chikwama ndipo chikwamacho anachilowetsa m’thumba la malaya ake. Kino anatuluka m’nyumba mwake ndi mdidi. Juana ankamulondola 28