Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale | Page 30

Ngale pang’ono. “Kuteroko dokotala uja amadziwa!” anadziyankhulira yekha Kino. Iye ankakumbukira mankhwala oyera omwe anamupatsa aja. Juana anayamba kuyimba Nyimbo ya Banja Lake pofuna kutonthoza Coyotito yemwe anali mu ululu wowopsa, ndipo ankachita zimenezi kwinaku akumususuza kuti agone. Nyimbo yoyipa inayamba kumveka kwambiri m’makutu mwa Kino moti zinali zovuta kuti amve nyimbo yomwe Jua- na ankatonthozera mwana ija. Atamaliza kumwa tiyi wake, dokotala uja anaponya mkamwa ka- chidutswa komaliza ka bisiketi yemwe ankamwera. Kenako anapukuta manja ake ndi kathawelo n’kuyang’ananso pankono wake. Ndiyeno anadzuka n’kunyamula chikwama chake n’kuwuyamba wa kunyumba kwa Kino. Ankadziwa kuti bomba limene anatchera laphulika. Nkhani ya matenda a Coyotito inafala mofulumira kwambiri. Ena ankanena kuti, “Mwawona, mwayitu umabweretsa mavuto ambiri.” Ena ankavomereza zimenezi n’kumalowera kunyumba kwa Kino kuti akawone kuti mwanayo ali bwanji. Posakhalitsa pakhomopo panadza- dza anthu. Iwo anangoyima n’kumakambirana za kuchuluka kwa mavuto amene amabwera munthu akangopeza kachisangalalo kochepa. Ena atawona mmene mwanayo analili anayamba kunena kuti, “Tiyeni tingosiya zonse m’manja mwa Mulungu.” Dokotala uja anatulukira mapewa ali m’mwamba. Atangofika anan- yamula Coyotito n’kuyamba kumuyang’ana mosamala, kenako ana- mugunditsa dzanja lake pachipumi kuti awone mmene thupi lake linka- tenthera ndipo anati: “Poyizoni uja wayamba kugwira ntchito yake. Ko- ma ndikuganiza kuti ndikhoza kulimbana naye.” Atatero anayitanitsa madzi oti asungunuliremo mankhwala. Atamaliza kupanga nsakanizo wakewo anamutsegula pakamwa n’kumupungulira mankhwalawo ku- khosi ndipo Coyotito anayamba kulira. Posakhalitsa anayamba kusanza moyipa moti akanapitirizabe akanasanza matumbo. “Monga ndinakuwuzirani kale, muli ndi mwayi kuti ndimadziwa mankhwala a poyizoni wapheterere, kupanda apo—“ anatero diso lili pamtunda pofuna kuwathandiza kudziwa kuwopsa kolambalala doko- tala mwana wawo atalumidwa ndi pheterere. 24