Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale | Page 27

Ngale mbiri ana anga.” Kenako anatembenuka n’kumapita. Anthu aja anapitiriza kufumuka m’modzim’modzi n’kumapita m’makwawo. Juana anayamba kukonza chakudya chamadzulo. Anthu onse aja atapita, Kino anadzuka n’kukayima pakhonde. Monga ankachitira nthawi zonse, akayima pamalowa ankatha kumva fungo la zomwe zinkaphikidwa m’makomo oyandikira. Ankathanso kumva kam- phepo kotsitsimula kakumadzulo. Koma madzulowa, Kino ankango- dzimva ngati ali yekhayekha. Iye anafumbata ngale yake ija mwam- phamvu ndipo anayamba kuwona kuti akapusa anthu akhoza kumuy- eretsa m’maso. Kino ankatha kumva Juana akuwumba mikate n’kumayiyika m’chi- waya. Koma maganizo ake sanali pa zimenezo. Iye ankaganizira mmene angagwetsere makoma komanso zopinga zonse zomwe zinkafuna ku- mutsekereza. Ankawona kuti akufunika kumenya nkhondo yoteteza tsogolo la banja lake. Posakhalitsa Kino anawona anthu awiri akubwera molunjika kunyumba kwake. Anali dokotala ndi wantchito wake uja. Dokotalayo anangofikira kunena kuti, “Ineyo kunalibe pamene mu- nabwera m’mawa uja. Ndiye ndabwera kuti ndidzawone kuti mwana ali bwanji komanso kuti ndidzamupatse chithandizo chamankhwala.” Kino anamva kuwawa mumtima mwake chifukwa cha mawu ame- newa. Kunena zowona, kumeneku kunali kumutsutsula pachilonda chomwe chinali chitangoyamba kumene kupola. Akaganizira chipongwe chomwe dokotalayu anamuchita m’mawa uja, ankamva ululu wowopsa mumtima mwake. “Musadandawule, wayamba kupeza bwino tsopano,” anatero Kino. Dokotalayo anamwetulira mwawudyabolosi, maso ake akuthwa ali ngwe-e. “Ukudziwa mnzanga, nthawi zinatu poyizoni wapheterere amachita zinthu modabwitsa.” Kenako anayendetsa nkono n’kubweretsa kutsogo- lo chikwama chomwe ankayikamo zipangizo zake zogwirira ntchito. Iye ankadziwa bwino mmene anthu amtundu wa Kino ankakondera kuwona zipangizo za dokotala. 21