Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale | Page 26

Ngale Azibambo omwe anatsalira pakhomopo anavula zisoti zawo ndipo anapereka mpata kuti Bambo Mfumu adutse. Nawonso azimayi anazyo- likira pansi popereka ulemu kwa wansembeyo. Kino ndi Juan Tomas anayimirira ndipo wansembeyo analowa m’nyumba. Wansembeyo anali wachikulire ndithu moti kumutu kwake kunali kutachita phulusa. Nalonso khungu lake linali lokhwinyata. Ndi maso ake okha omwe anali akuthwa kuposa mpeni. Wansembeyo ankawona anthu onsewa ngati ana ake, ndipo ankawayankhulanso ngati ana. “Kino,” anatero wansembeyo chapansipansi, “unapatsidwa dzina la munthu wofunika kwambiri yemwe ndi bambo wa tchalitchi chathu.” Mawu a wansembeyo ankamveka ngati akuchititsa mwambo wamapemphero. “Munthu ameneyu anachita zinthu zambiri zam- phamvu ndipo zonse zimene anachita zinalembedwa m’mabuku.” Maso a Kino anapita pamene panali mwana wake Coyotito. Mumti- ma mwake ankangoti, “Tsiku lina mwana wangayu adzadziwa zimene zimapezeka m’mabuku. Tidzawona ngati zimene akunenazi zili zowona kapena zabodza.” Nyimbo ya ngale ija inachoka m’mutu mwake ndipo munayamba kumveka nyimbo yoyipa. Kenako wansembe uja anati: “Ndamva zoti wapeza ngale yamtengo wapatali.” Kino anatambasula dzanja lake n’kumuwonetsa ngale ija. Wanse- mbeyo anadzidzimuka ndi kukula kwake. Kenako anatsukuluza ku- khosi n’kunena kuti: “Sindikukayikira kuti ukumbukira Ambuye Wa- kumwamba amene wakupatsa mphatso imeneyi. Nanga munthu ama- luma dzanja limene limamudyetsa ngati? Theka la ndalama utapezeyo ukufunika kumupatsa Ambuye!” Kino sanayankhe kanthu. Juana ndi amene anayankha kuti, “Musadandawule Bambo Mfumu. Titakhala pansi tinaganiza zoti timan- gitse ukwati wathu kutchalitchi. Komanso tikufuna kupereka kenakake ngati mphatso kwa Mulungu wathu. Kino amati tichita zimenezi tikangogulitsa ngaleyi.” “N’zosangalatsa kuti mwasankha kuchita zinthu mwanzeru chon- cho,” anatero wansembeyo. “Mukatero Mulungu akudalitsani kwa - 20