Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale | Page 24

Ngale nkhope yake pobisira anthuwo chimwemwe chimene anali nacho. Kwa Kino, kuwala kosangalatsa kwa ngaleyo kunkabweretsa maloto ambi- rimbiri. Ankatha kuwona akukwanitsa kuchita zonse zimene ankalakala- ka. Kenako anayankhula chapansipansi kuti, “Tikangogulitsa ngaleyi tikamangitsa banja lathu kutchalitchi! Tsopano tikhoza kukwanitsa kuli- pira wansembe kuti atidalitsire ukwati wathu!” Ankathanso kuwona mmene azidzatchenera. Ankawona Juana ata- vala siketi yatsopano, nsapato yodula ili phuliphuli kuphazi. Nayenso ankadziwona atatotokola nsanza zonse za umphawi wake n’kuvala zovala zapamwamba, chisoti chatsopano komanso nsapato mbambande. Akaganizira za mwana wake Coyotito, ankamuwona atavala kasuti kodula kochokera ku Amerika komanso atavala kachisoti kumutu. Mo- sadziwa, anangozindikira pakamwa pake patatseguka n’kunena kuti, “Tigula zovala zatsopano!” Maloto amenewa anabalanso anzake moti Kino anayamba kugan- izira zinthu zinanso zing’onozing’ono zomwe ankazilakalaka pamoyo wake. Ankafuna zipangizo zatsopano za ntchito yake yawusodzi ko- manso ankafuna atakhala ndi mfuti. Popeza ndalama zimayankhula, Ki- no ankawona kuti palibe chingamulepheretse kupeza zinthu zimenezi. “Ndigula mfuti,” anatero Kino, “Ndikangogulitsa ngaleyi ndigula mfuti!” Ndi mfutiyi yomwe inabweretsa maloto enanso aakulu kwambiri. Kunena zowona anthu sakhala okhutira ndi zimene ali nazo. Ngati uta- wapatsa chinthu chimene akufuna, amayambanso kulakalaka china. Ko- ma mtima umenewu ndi woyipa kwambiri chifukwa umachititsa kuti anthu azikhala adyera komanso ansanje ndipo ndi umene umasiyanitsa anthu ndi zinyama. Zinyama zimakhala zokhutira ndi zinthu zochepa zimene zimapeza pomwe anthu amafuna zonse zikhale zawo. Amafuna kupezeratu zinthu zamtsogolo ndipo ena amafika mpaka poyiwala nazo mabanja awo. Amangokhalira kuwunjika zinthu padzikoli mpaka kud- zalowa m’manda. Tikabwerera pa nkhani ya maloto ija, anthu amawona kuti si bwino kumalota mosinira. Safuna kumalota akudya masamba, mwayi woti akhoza kumalota akudya nyama ulipo. Anthu aja ankangomumvetsera Kino akufotokoza maloto ake ndipo 18