Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale | Page 17

Ngale zili pepeya. Anthu omwe anali panjapo anamva chisoni kwambiri ndi zimenezi. Palibe chimene akanachita kuti amuthandize. Opemphapempha aja anabwerera n’kukakhala pamgodi wawo, ndipo ena onse anabalalika n’kumalowera m’makwawo. Kwa nthawi yayitali, Kino anayimabe panja paja limodzi ndi mkazi wake Juana. Atawona kuti zinthu zavuta, anavalanso chisoti chake chija kumutu. Chifukwa chopsa mtima, anamenya mwamphamvu geti ndi chibakera chake n’kuyang’ana pansi asakukhulupirira chipongwe chime- ne dokotalayo anawachitira. Posakhalitsa magazi anayamba kuyendere- ra pankono wake n’kumakhera pansi. 11