Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale | Page 11

Ngale Coyotito ankangoseka kwinaku akuyang’ana pheterereyo ndipo anatukula nkono wake kuti amugwire. Chilombocho chinadabwa ndi zimenezi moti chinayamba kuyendetsa mchira wake kuti chilume. Kino ankamva Juana akunena mawu othamangitsa tsokalo kum- buyo kwake. Ndiyeno pamene ankatambasula dzanja lake kuti amukupe, Coyotito anaseka kwambiri mpaka kugwedeza chingwe chija moti pheterereyo anayamba kugwa. Zimene zinachitika pamenepo zinali zowopsa kwambiri. Kino ana- dumpha ngati chule kuti awakhe phetetereyo koma anamuphonya ndipo anagwera paphewa pa Coyotito n’kuzika mbola yake pamenepo. Kino anatola pheterereyo nsangansanga n’kuyamba kumutikita ndi zala zake. Kenako anamutsitsitizira pansi ndi chala chake. Pa nthawiyi Coyo- tito anali akulira mosatonthozeka. Kino anapitirizabe kutikita mdani wakeyo mpaka atatheratu moti pamalowo sipankawonekanso zoti panali chamoyo. Juana ananyamula Coyotito m’manja mwake. Atangowona kuti malo amene pheterere uja analuma akufiyira, nthawi yomweyo anayamba kutsopapo n’kumalavulira pansi. Coyotito analira mowopsa. Kino ankangoti zungulizunguli, kusowa pogwira. Kulira kwa mwa- naku kunachititsa kuti anthu a nyumba zapafupi adabwe moti anaya- mba kukhamukira kunyumbako. Mchimwene wa Kino, dzina lake Juan Tomas komanso mkazi wake wonenepa kwambiri, dzina lake Apolonia, anatulukira limodzi ndi ana awo anayi. Anthuwa anayima pakhomo la nyumba ya Kino ndipo kumbuyo kwawo kunali anthu enanso ambi- rimbiri omwe ankasuzumira m’nyumbamo. Kamwana kena kankakwa- wa n’kumadutsa mphechepeche mwa anthu kuti kakawone chomwe chinkachitika m’nyumbamo. Amene anali kutsogolo ankapereka uthe- nga wa zimene zachitika kwa amene anali kumbuyo kwawo. “Ndi pheterere. Mwana walumidwa ndi pheterere,” anatero wina. Juana anali atapumira kaye kutsopa poyizoni uja ndipo anakwanitsa kuchotsapo wambiri ndithu. Pamalopo panali patakula pang’ono chifu- kwa chakutsopako. Komabe kufiyira kuja kunapitirizabe kufalikira. An- thu onse omwe anabwera pamalowa ankadziwa bwino kuwopsa kwa 5