Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale 2 | Page 8

Ngale yomwe inkalira m’mutu mwake. N’kutheka kuti anthu onse amtundu wake ankachitanso chimodzimodzi. Zimamveka kuti m’mbuyomo anthu amenewa anali akatswiri opeka nyimbo moti chilichonse chimene awona, kuganiza, kuchita, kapena kumva, ankachipekera nyimbo. Koma limenelo linali makedzana. N’zowona kuti nyimbo zomwe anapeka zi- nali zikadalipo. Komabe, zikuwoneka kuti mavuto owopsa omwe anka- kumana nawo anachititsa kuti asamapekenso nyimbo zina. Komabe, ali- yense ankatha kukhala ndi nyimbo yake yomwe ankayimva m’mutu mwake. Ndi mmenenso zinalili ndi Kino. Akakhala pansi n’kumaganiza, m’mutu mwake munkamveka nyimbo zosiyanasiyana. Nyimbo yomwe inkamveka m’mutu mwake m’mawawu inali yosangalatsa kwambiri ndipo zikanakhala kuti akuyiyimba motulutsa mawu, bwenzi akuyitch- ula kuti Nyimbo ya Banja Lake. Kino anali atafunda ndi kumutu komwe chifukwa cha mphepo yozi- zira yomwe inkawomba m’mawawo. Posakhalitsa Juana anadzuka mwakachetechete n’kupita pamene panali bokosi la Coyotito ndipo an- awerama n’kuyamba kumuyankhula chapansipansi. Coyotito anayan- g’ana mayi akewo ndipo anatsekanso maso ake n’kugona tulo. Kenako Juana anapita kukakoleza moto. Anafukula khala paphulusa n’kuyamba kulipemerera kwinaku akuthyolerapo timatsatsa mpaka moto unakol- era. Kino nayenso anadzuka bulangete lili kumutu n’kuvala nkhwayira zake, kenako anatuluka panja kuti akawone dzuwa likutuluka. Atatulu- ka ananjuta pakhonde n’kumayang’ana mtambo wachikasu womwe un- kawoneka panyanja. Moto anakoleza Juana uja unali lawilawi moti un- kachititsa kuti kuwala kuzivinavina kunsana kwake. Kachilombo kena kowuluka kanalowa m’nyumbamo n’kumakazungulirazungulira pafupi ndi motowo. Pamenepo Nyimbo ya Banja Lake inayambanso kumveka m’mutu mwake. Iye anamva mkazi wake akupera tirigu pamphero kuti apange mikate ya mfwisuro. Posakhalitsa dzuwa linayamba kumwetulira panyanja ndipo mdima wonse unabalalika. Kuwala kwa dzuwalo kunayamba kuwonjezereka pang’onopang’ono moti cheza chake chinamwazikira mbali zonse n’ku- walitsa nyanjayo ngati galasi. Kino anaphimba nkhope yake kuti 2