Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale 2 | Page 70

Bonwell Kadyankena Rodgers Bukuli linalembedwa ndi Bambo John Steinbeck mu 1936 ndipo lamasu- liridwa m’Chichewa ndi Bonwell Kadyankena Rodgers. Bukuli limaso- nyeza kuti pali anthu ena omwe amangofuna kuti zabwino zonse zikhale zawo. Limasonyezanso mtima wachinyengo komanso wadyera umene ambiri ali nawo, mtima womakonda munthu kapena kumuchitira za- bwino akawona kuti apindulapo kenakake. Anthu amenewa amatha- mangira munthu zovala zili yambakatayambakata kuti anthu aziti ndi Asamaliya achifundo, koma pansi pamtima ali ndi zolinga zawo zomwe akufuna kukwaniritsa. Amakondanso kuchita ubwenzi ndi anthu ole- mera ndipo akawona munthu wosawuka akuvutika, amangomuyang’a- na akuwola ndi mavuto podziwa kuti akamuthandiza sapindulapo chili- chonse. Ngati mukufuna kuwadziwa anthu amenewa ingoyang’anani anthu amene akuzungulirani. Kenako dzifunseni kuti, ‘Kodi anthu ame- newa amandikonda chifukwa chiyani?’ Ngati amakukondani chifukwa cha galimoto yanu, ndalama, maphunziro kapena chinachake chimene muli nacho, dziwani kuti mabwenzi amenewo akutayitsani nthawi.