Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale 2 | Page 7

Ngale Anthu a m’mudzi wina amakonda kufotokozerana nkhani ya munthu wina yemwe anapeza ngale yamtengo wapatali n’kuyitaya itamuwonetsa mavuto. Dzina la munthuyu linali Kino, ndipo mkazi wake anali Juana. Banjali linali ndi mwana m’modzi yemwe dzina lake linali Coyotito. Ndiye popeza nkhaniyi yakhala ikukambidwa mobwerezabwereza, anthu anafika poyiloweza moti amatha kuyinena ngakhale atadzidzimuka kutulo. Monga zimakhalira ndi nkhani zomwe anthu akuzidziwa bwino, ndikulonjeza kuti sindichulukitsa gaga kapena kubwitikiza madeya m’diwa. Ndingokufotokozerani ndendende mmene zinachitikira. Ngati nkhaniyi ili fanizo, aliyense apeze yekha tanthawuzo lake komanso awone mmene ikukhudzira moyo wake. Imayamba motere . . . Gawo 1 Kino anadzidzimuka kunja kusanachesetse. Nyenyezi zinali zikuwalabe kuthambo ndipo zizindikiro zoti kunja kukucha zinali zitayamba kuwonekera. Pa nthawiyi atambala anali atayamba kale kulira ndipo na- zonso nkhumba zolawira zinkayendayenda m’madzala n’kumafufuza chakudya chosadziwika chomwe chimazithandiza kuti zinenepe. Panja pa nyumba ya Kino, yomwe tinganene kuti inali chisakasa chopangidwa ndi mitengo komanso udzu, pankamveka kulira kwa mbalame zolawira kotola mphutsi. Pamene ankatsegula maso ake, Kino anawona kuwala komwe kunkalowera m’nyumbayi kudzera m’mipata yomwe inali kukhomo ndipo anayendetsa maso n’kuyang’ana bokosi lomwe munali mwana wake, Coyotito. Kabokosiko kanamangiriridwa kudenga ndi zingwe ziwiri ndipo kankalendewera m’malere. Kino anatembenukira mkazi wake Juana, yemwe anagona pambali pake atafunda shawelo. Nthawi zonse Kino akamadzuka ankapeza mkazi wakeyu akumuyang’ana. Kino sankakumbukira tsiku limene anamuwonapo ali m’tulo. Pamene m’maso mwake munkayera, anayamba kumva kulira kwa mafunde omwe ankamenya m’mbali mwa gombe. Kino ankakhutira ndi mmene zinthu zinkayendera pamoyo wake ndipo ankawona kuti zonse zili tayale. Posakhalitsa anatsekanso maso ake n’kumamvetsera nyimbo 1