Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale 2 | Page 64

Ngale Pa nthawiyi, m’mutu mwa Kino munkamveka nyimbo yamdani. Koma chapansipansi pankamvekanso nyimbo ina. Inali Nyimbo ya Banja Lake. Pamene ankatsetsereka nyimbo yachiwiriyi inayamba kukula mphamvu moti inachititsa kuti alimbe mtima ngati mkango. Kino anayenda mwakachetechete kudutsa pamwala wotererawo. Zi- namutengera nthawi yayitali kuti akafike pansi paja. Mtima wake unkangoti phaphapha ndipo manja ndi nkhope yake zinali thukuta lo- khalokha. Atafika pansi, anabisala kuseri kwa mtengo wina kuti asonkhanitse mphamvu. Diso lake linangoti ga pa munthu anali ndi mfuti uja. Tsopano Kino anali pafupi kwambiri ndi adani akewo. Chifukwa chamdima, iye anayesetsa kukumbukira kutalika kwa mtunda umene unali pakati pa iyeyo ndi adani akewo. Mwamwayi munthu ankayan- g’anira anzake uja chibaba chinamugwira ndipo anatenga tcheso n’kulikhwetchetsa ku chikalakala kuti ayatse fodya wake. Zimene Kino anawona pamenepo zinamuthandiza kudziwa malo enieni amene mun- thuyo anali. Ndi awiri ankagona aja omwe sanawawone. Kenako anayang’ana kum’mawa ndipo anawona kuti mwezi uja wangotsala pang’ono kutulula. Iye ankayenera kuchitapo kanthu mweziwu usana- tuluke, apo bi-i zinthu zikanamusokonekera. Chidwi chake chonse chi- nali pa munthu anali ndi mfutiyo. Kuwukira munthu ameneyu n’kumu- landa mfutiyo kukanatanthawuza chipulumutso kwa iye ndi banja lake. Choncho Kino sankafuna kuseweretsa mwayi umenewu. Mwakachetechete anagwira mpeni wake mwamphamvu, koma anachedwa. Tikutero chifukwa pa nthawiyi mpamene mwezi uja un- atuluka. Izi zitachitika, Kino anabwereranso kuseri kwa mtengo. Mwezi wake unkawala ngati chikoloboyi chakutha mafuta. Komabe unathandiza Kino kuwona anthu aja bwinobwino. Posakhalitsa m’modzi wa awiri ankagona aja anadzidzimuka ndipo anafunsa kuti, “N’chiyani chikuliracho?” “Sindikudziwa,” anatero anali ndi mfuti uja. “Ndamva ngati kulira kwa mwana.” “Ayi si mwana, ndi nyama imeneyo. Palitu nyama zina zomwe zima - 58