Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale 2 | Page 63

Ngale wanga! Undikhululukire pa zimene ndinakulakwirapo m’mbuyomu.” Kenako anapumira pang’ono n’kunena kuti, “Ngati nditatsika anthuwa n’kundiposa mphamvu, iweyo ungokhala chete. Sindikukayikira kuti akagwira ineyo kapena kundipha atenga ngaleyi n’kubwerera. Zikatero iweyo utsike n’kuthawira ku Loreto.” Juana anali atagwira dzanja la mwamuna wakeyo ndipo atangomva mawu amenewa anayamba malungo. “Ndikuyenera kutero mkazi wanga,” anatero Kino. “Kupanda kutero, mawa kukamacha atigwira ndipo tikhoza kufa imfa yowawa zedi.” Juana ankanjenjemera kwambiri tsopano, komabe anadzilimbitsa n’kunena kuti, “Mulungu akutsogolereni.” Kino anayang’ana mkazi wakeyo kwa kanthawi. Zina zimangochi- tika, koma kunena zowona anthuwa ankakondanadi, kaya pamavuto kapena pamtendere. Aliyense anali wokonzeka kupereka moyo wake kuti apulumutse banja lake. Kino anayendetsa dzanja lake n’kusisita mwana wake Coyotito. Kenako nkhope yake itakutidwa ndi chisoni, anagwira mwachikondi tsaya la mkazi wakeyo. Zinali zolilitsa zedi. Posakhalitsa Juana anawona Kino akuvula malaya ake oyera aja. Imeneyi inali nzeru chifukwa thupi lake lachimwenye likanamuteteza kusiyana ndi malaya oyerawo, omwe ankawonekera patali kwambiri. Juana anawona mwamuna wakeyo akukoleka chingwe cha mpeni wawukulu uja m’khosi ndipo mpeniwo anawuberekera kumbuyo. Zime- nezi zinachititsa kuti manja ake onse azigwira ntchito zina. Atangotulu- ka n’kusiyana ndi mkazi wakeyo sanabwererenso. Juana ankangow- onerera mwamuna wakeyo akupita ku Gologota kukapachikidwa ndipo palibe chimene akanachita. Coyotito anali atagona. Zimenezi zinapereka mpata kwa Juana kuti azipempherera mwamuna wake kuti Mulungu amuteteze. Kino anayamba kutsetsereka pang’onopang’ono kuchokera panali mapanga paja. Iye ankakwawa mpeni wake uli kumbuyo ndipo izi zi- nathandiza kuti usachite phokoso pomenya mwalawo n’kumugwiritsa. 57