Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale 2 | Page 53

Ngale Gawo 6 Mphepo inapitirizabe kuwomba mwamphamvu ndipo inkawulutsa zitsotso, mchenga komanso timiyala tomwe tinkawamenya m’mapazi komanso kumaso. Kino ndi Juana anagwira mwamphamvu akatundu awo kwinaku akuponya phazi patsogolo n’kumalowa mkati mwen- imweni mwa mdima. Anthu awiriwo anayenda mosamala kwambiri pamene ankadutsa m’tawuni ija. Kenako anatsata nyenyezi ina ya- kumpoto. Atayenda pang’ono anapeza nsewu wakale kwambiri wotulu- ka m’tawuniyi. Nsewu umenewu unali wamchenga ndipo unkalowera ku Loreto. Kino ankatha kumva mchenga ukumumenya m’mapazi ndipo zime- nezi zinkamulimbitsa mtima chifukwa ankadziwa kuti anthu owasa- kasaka sangathe kupeza madindo a mapazi awo. Kino ankangoyenda osayankhula ndipo Juana ankangomutsatira pambuyo. Zikuwoneka kuti Kino ankawopa kuyenda usiku. Koma patsikuli, ankangokhala ngati munthu wina. Mphepo inkawawomba kuchokera kumbuyo kwawo ndipo nyenyezi zinkawatsogolera. Banjali linakoka phazi ndipo linayenda mtunda wawutali osakumana ndi munthu ali- yense. Kenako mwezi unatuluka kumanja kwawo. Utangotuluka, mphe- po ija inasiya kuwomba ndipo kunja kunangoti zii. Tsopano ankatha kuwona munsewu muja bwinobwino. Nsewuwo unali ndi mchenga wambiri ndipo pamchengawo panadindika mateyala. Kungochokera pamenepa kumene ankalowerako ankasiya madindo a mapazi. Koma zimenezi sizinali zodandawulitsa kwenikweni chifukwa anali atatha mtunda tsopano. Kino ankayenda mosamala n’kumaponda momwe munali madindo a mateyalamo, ndipo Juana ankamutsatira pambuyo pake. Anayenda usiku wonse, ndipo sanapume. Pa nthawi ina Coyotito anadzuka. Juana anayamba kumutonthoza ndipo kenako anagonanso. Koma zowopsa za usiku zinali zitawazungulira. Iwo anayamba kumva kulira kwa nyama zolusa za usiku zomwe zinkaseka kuseri kwa miten- go. Mbalame zawusiku zinkawuluka zikuyimba nyimbo zawusiku. Ndipo ulendo wina nyama zina zazikulu zinadutsa chapafupi. Kino 47