Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale 2 | Page 5

Bukuli linalembedwa ndi Bambo John Steinbeck mu 1936 ndipo lamasu- liridwa m’Chichewa ndi Bonwell Kadyankena Rodgers. Bukuli limaso- nyeza kuti pali anthu ena omwe amangofuna kuti zabwino zonse zikhale zawo. Limasonyezanso mtima wachinyengo komanso wadyera umene ambiri ali nawo, mtima womakonda munthu kapena kumuchitira za- bwino akawona kuti apindulapo kenakake. Anthu amenewa amatha- mangira munthu zovala zili yambakatayambakata kuti anthu aziti ndi Asamaliya achifundo, koma pansi pamtima ali ndi zolinga zawo zomwe akufuna kukwaniritsa. Amakondanso kuchita ubwenzi ndi anthu ole- mera ndipo akawona munthu wosawuka akuvutika, amangomuyang’a- na akuwola ndi mavuto podziwa kuti akamuthandiza sapindulapo chili- chonse. Ngati mukufuna kuwadziwa anthu amenewa ingoyang’anani anthu amene akuzungulirani. Kenako dzifunseni kuti, ‘Kodi anthu ame- newa amandikonda chifukwa chiyani?’ Ngati amakukondani chifukwa cha galimoto yanu, ndalama, maphunziro kapena chinachake chimene muli nacho, dziwani kuti mabwenzi amenewo akutayitsani nthawi. Language Clarification Program: Kubwezeretsa zilembo zopanda liwu (consonants) m’malo omwe zilembo za liwu (vowels) zatsatana, zomwe malinga ndi malamulo a Chichewa ndi zosayenera. Bukuli ndi loyeserera pa nkhaniyi ndipo labwezeretsa chilembo cha “w” komanso cha “y” m’malo onse omwe chimafu- nikira kukhalapo, kupatulapo mawu ena apadera komanso obwerekera m’zinenero zina omwe samveka bwino akawonjezeredwa zilembozi. Zikuwoneka kuti chidule chowonongetsa zinthu n’chomwe chinachotsetsa zilembozi. Anthu anazolowera kulemba mwachidule chonchi moti sawona vuto zilembo za liwu kundondozana. Werengani bukuli kuti muwone mmene mawu a Chichewa amakongolera akalembedwa m’njira yolondolayi. Mfundo yofunika kuyiganizira ndi yakuti zolakwika sizisanduka zolondola kokha chifukwa choti anthu ambiri anazizolowera.