Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale 2 | Page 49

Ngale Kino anatola mpeni wake n’kutsetserekera kudoko. Koma anadzi- dzimuka atazindikira kuti bwato lawo labowoledwa ndipo madzi anali nde-e m’bwatolo. Zikuwoneka kuti amene anachita zimenezi ndi mun- thu wina wamtopola yemwe ankafuna kuti Kino asowe chokwera ak- amapita kokagulitsa ngale yake ija. Apa zinali zowonekeratu kuti mdima wamavuto wayamba kukuta banja lake. Nyimbo yoyipa inayamba kumveka kwambiri m’mutu mwake. Iye sanakhulupirire kuwona bwato lomwe agogo ake anagula litabowoledwa. Kunena zowona kumeneku kunali kuyipa kwakukulu. N’zowona kuti kupha munthu n’koyipa. Ko- mabe kuderali, kubowola bwato la mnzako kunali koyipa zedi chifukwa bwato linali moyo wa munthuyo. Komanso kodi munthu wamtopolayo ankalimbana bwanji ndi bwato lomwe silinamuyambe? Kino anangosan- duka chinyama tsopano. Chimene ankafunika kuchita apa chinali kute- teza moyo wake komanso wa banja lake. Ululu wa pachipumi pake uja unali utabalalikiratu. Atawona malodza anachitikawo, nthawi yomweyo anayamba kuthamangira kunyumba kwake. Kino sanali woyipa mtima moti n’kufika pothawa ndi bwato la munthu wina. Iye anathamanga kwinaku akufufuza pamene anasunga ngale yake ija. Atayipeza, anayambanso kufufuza mpeni wake womwe anawubisa m’malaya. Atayandikira kunyumba kwake, Kino anawona kuwala kodabwitsa. Ataponya maso anawona nyumba yake ikunyeka ndi moto mkati mwa mdima wa usikuwo. Kino ankadziwa kuti palibe chimene munthu ama- pulumutsa nyumba yomangidwa ndi mitengo komanso udzu ikayamba kuyaka. Chomwe chimafunika kupumumutsa poteropo ndi moyo wa ana komanso anthu ena omwe ali m’nyumbapo. Pamene ankathamanga kumalowera kunyumbako, anangowona Juana watulukira. Iye anali atanyamula Coyotito. Juana anali ndi mantha aakulu moti ankalephera ngakhale kutonthoza Coyotito yemwe ankalira m’manja mwake. “Ndi ndani wachita zimenezi?” anafunsa Kino. “Sindikudziwa,” anatero Juana. Anthu a nyumba zoyandikira anali atayamba kale kutuluka m’nyumba zawo. Posakhalitsa anayamba kulimbana ndi motowo kuti usawuluke kapena kufika pokula moti n’kuyatsanso nyumba zawo. 43