Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale 2 | Page 45

Ngale peto. Palibe amene akuyenera kutilanda mwayi umene tapeza.” Maso ake anayamba kuwoneka mofewa ndipo kenako anayika dzanja lake paphewa la Juana. “Usakayikire Juana,” anapitiriza Kino. “Ndine mwamuna. Mawa kukangocha titenga bwato lathu ndipo tiwoloka nyanjayi n’kudutsa ma- piri mpaka kukafika kumzinda wawukulu. Tipita iweyo ndi ineyo. Ku- meneko tikapeza ogula achilungamo. Usakayikire, ndine mwamuna ndi- kuteteza.” “Kino,” anatero Juana. “Komatu ndikuchita mantha. Mumadziwa kuti ngakhale mwamuna amatha kufa? Tiyeni tingoyitaya ngaleyi isanatiputitse mavuto.” “Basi khala chete,” anatero Kino mokwiya. “Ndakuwuza kale kuti ndine mwamuna! Usandisokosenso ndi nkhani imeneyi.” Juana atan- gomva mawu amenewa anakhala chete. “Tiye tizigona. Chakum’ban- dakucha tingobulika tiwuyambe. Kapenatu sukufuna titsagane?” “Ayi mwamuna wanga, ndipita nawo.” Atangonena mawu amenewa, Kino anayang’ana mkazi wakeyo mosangalala. Kenako anamugwira mwachikondi patsaya. “Tiye tigone pang’ono,” anatero Kino. 39