Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale 2 | Page 40

Ngale Kino anapsa mtima atamva zimenezi moti anamukwatula ngaleyo n’kuyiyikanso pakansanza kaja. Munthu wonenepa uja anayambanso kuyankhula ndipo anati, “Wawonatu mnzanga! Ndakupatsa mtengo wabwino zedi. Palibenso kwina kumene ungakagulitse ngale imeneyi pamtengo wongopereka ngati umenewu. Ndiye ukuti bwanji? Ndikupatse 1,000 pesos yako uz- ipita? Sindikuganizanso kuti uchita bobobo pamenepa chifukwa ukatero, ukhoza kunong’oneza bondo pamapeto pake!” anatero pamene Kino ankayika ngale yake m’thumba la malaya. “Ndinu anthu akuba kwabasi,” anatero Kino mokwiya. “Ndikhoza kungotayapo nthawi pano. Ndipita kukagulitsa ngale yangayi kumzinda wawukulu.” Tsopano ogula ngalewo anazindikira kuti mwayi wogula ngale yamtengo wapataliyo wawapulumuka m’manja moti munthu wonenepa uja anawonjezera mtengo ananena poyamba uja. Iye anati: “Chabwino, ndikugula 1,500.” Koma pamene ankanena zimenezi, Kino anali atatuluka kale panja. Pamene ankadutsa pakati pa gulu lomwe linali panjapo, anamva anthu akuyankhula zinthu zosiyanasiyana koma sanawasamale. Juana anamut- satira pambuyo pake chothamanga. Madzulo a tsiku limenelo, anthu oyandikana nawo nyumba aja analowa m’nyumba zawo n’kumadya mikate yawo. Iwo ankakambirana zimene zinachitika m’mawa wa tsikulo. Kunena zowona, nawonso anali asanawonepo ngale yayikulu ngati ya Kino ndipo ankadziwanso kuti ogulawo anali akatswiri pa nkhani yonena kuti ngale iyi ndi yabwino kapena ayi. “Ine ndikuwona kuti ogula aja sanachite kupangana kuti anene mi- tengo imene ija,” ankatero anthuwo. “Onse atatu amawona kuti ngale ija ndi yopanda ntchito.” “Koma mwina amanama! Ndani akudziwa, mwina anagundana mi- tu! Pajatu apawo ndi mizu ya kachere, amakumana pansi.” “Komatu ngati zilidi zowona ndiye kuti amangotibera tikamawagu- litsa ngale zathu.” 34