Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale 2 | Page 36

Ngale “Ndinamvadi,” anatero Kino. “Bambo ndi amene anandifotokozera nkhani imeneyi. Inali njira yabwino kwambiri, koma kungoti inali yo- semphana ndi mfundo zatchalitchi. Wansembe ananena zimenezi momveka bwino. Anati Mulungu sanakondwere ndi njira imeneyo chifukwa safuna kuti munthu asiye malo ake n’kumangoyendayenda ngati njoka. Anatsindika mfundo yakuti munthu akachita zosemphana ndi zimenezi amakumana ndi tsoka moti samakayikira kuti anthu ame- ne anatumidwawo anachita kulangidwa ndi Mulungu.” “Wansembe wathu uja amakondadi kunena zimenezi chaka chili- chonse,” anatero Juan Tomas. Anthu apachibalewa anatseka maso awo pang’ono. Iwowa komanso azigogo awo, ngakhalenso azigogo a azigogo awo anayamba kuchita zimenezi pamene alendo ochokera ku Spain anabwera kwawoku ndi mifuti n’kuyamba kuwawopseza. Ndipo pa zaka zonse zokwana 400 zimene alendowa anakhala kumeneku, anthuwa anaphunzira njira imodzi yokha yodzitetezera. Njira yake inali kutseka maso komanso pa- kamwa pawo. Kulimbana ndi anthu amenewa kunali kuyika moyo pa- chiswe moti ngati ukufuna kukhala ndi moyo wawutali, nkhani zina un- kangofunika kuzimwera madzi n’kuziyiwala. Khamu la anthu lija linangoti nyomi, kuwalondola. Linkadziwa bwinobwino kufunika kwa tsikuli. Posakhalitsa anatulukira m’tawuni, ndipo mofanana ndi poyamba paja, opemphapempha amene ankakhala patsogolo pa tchalitchi chija anawalondola. Anthu ogulitsa m’magolo- sale anawaperekeza ndi maso. Nawonso ogulitsa m’mashopu anatseke- ratu chifukwa chosowa makasitomala ndipo anatsata Kino kogulitsa ngale yake. Nkhani ya kubwera kwa khamu la anthuli inafika ku mawofesi a ogula ngale aja. Iwo anachotsa ngale zawo n’kuzibisa. Sankafuna kuti Kino azidzayerekeza ngale yake yamtengo wapataliyo ndi ngale zawo zosalongosokazo. Mu ofesi imene Kino anasankha kukagulitsa ngale yake, munali munthu wina wonenepa ndipo anakhala pampando n’kumaseweretsa ndalama yasiliva. Nkhope yake inkawoneka yachifundo, ndipo maso ake anali awubwenzi. Iye anasiya chitseko cha ofesi yake chotsegula kuti 30