Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale 2 | Page 29

Ngale mbenukira Kino n’kumuwuza kuti, “Ndikuganiza kuti poyizoni yemwe ali m’thupi mwa mwanayu ayamba kuluma pakangotha ola limodzi. Ko- mabe, mankhwala amene ndamupatsawa amuthandiza kwambiri. Ndi- bweranso pakatha ola limodzi kuti ndidzawone kuti zikuyenda bwanji. Muli ndi mwayi kuti ndabwera pa nthawi yake, ndikanangochedwa pang’ono, zinthu sizikanakhala bwino moti moyo wa mwana wanuyu ukapanga phfu-u-u-u . . .” anatero dokotalayo pakamwa pake ponenepa patafufuma ndi mpweya poyerekezera mmene moyo wa mwanayo uka- naphulikira. Atangomaliza mawu amenewa ananyamuka n’kumapita. Juana limodzi ndi mwamuna wake anayamba kuyang’ana Coyotito mwamantha zedi komanso momumvera chisoni. Kino ananyamula dzanja lake kuti atsegule chikope cha Coyotito, koma anazindikira kuti ngale ija inali idakali m’dzanjalo. Kenako anapita pakabokosi komwe kanali pafupi ndi khoma n’kukatengamo chigamba n’kukutira ngaleyo. Atatero anapita pakona ya nyumbayo n’kukakumba kadzenje pomwe anayikapo ngaleyo n’kukwirira. Dokotala uja anayenda khathaphyakhathapya mpaka kwawo ndipo atangofika anakhala pampando wake wawofuwofu n’kuyamba kuyang’ana wotchi yake yapankono. Wantchito wake uja anamubwer- etsara tiyi ndi mabisiketi, ndipo dokotalayo anayamba kumupyontha. Madzulowa anthu oyandikira nyumba ya Kino ankakambirana zo- khudza Kino ndi ngale yake ija. Iwo ankayerekezera ndi zala zawo ku- kula kwa ngaleyo. Ankawuzana mmene ngaleyo ilili yokongola ko- manso mmene ingathandizire kuti Kino ndi Juana avuwuke mu umphawi n’kuyamba kuwoneka ngati anthu. Anthuwa ankadziwa chifu- kwa chake dokotala uja anabwera kunyumba kwa Kino. Ankadziwanso zimene zinali m’maganizo mwake. Madzulo umenewo Kino ndi mkazi wake anadya mikate yawo n’ku- khuta. Kenako Kino anapichira fodya wake n’kuyamba kusuta. Koma mwadzidzidzi, Juana anayitana mozula mtima: “Kino!” Atamva kuyitanako, Kino anadzambatuka n’kupita pamene panali mkazi wakeyo. Iye anadziwa kuti zinthu sizili bwino atawona mantha omwe Juana anali nawo pamene ankayang’ana Coyotito. Nkhope ya mwanayo inali itafiyira psu-u, ndipo zinali zowonekeratu kuti sali bwino ngakhale 23