Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale 2 | Page 28

Ngale “Nthawi zina,” anapitiriza motero dokotalayo, “munthu akalumid- wa ndi pheterere amawoneka ngati akuchira. Koma kenako amadzidzi- muka mwendo, diso kapena nsana wake zitawonongeka. Sindikuganiza kuti ukufuna kuti zimenezi zichitikire mwana wako. Mwamwayi ineyo ndimadziwa bwino mankwala a poyizoni wapheterere.” Kino anayamba kuchita mantha. Iye ankawona kuti dokotalayo ndi amene amadziwa zambiri zokhudza zachipatala. Ankadziwanso kuti do- kotalayo anaphunzira ndipo amadziwa bwino zomwe zimapezeka m’mabuku. Kino sankafuna kuti Coyotito adzakule wopanda mwendo, diso kapena nsana. Choncho analowa m’nyumba ndipo dokotalayo ana- mutsatira. Juana anasiya kaye kuphika n’kuyang’ana kumbali. Dokotalayo anapita pafupi naye n’kutambasula manja kuti anyamule Coyotito. Ko- ma Juana anakumbatira mwana wakeyo mwamphamvu kwinaku aku- yang’ana mwamuna wake. Kino anamuwuza ndi maso kuti apereke mwanayo ndipo anachitadi zomwezo. Dokotalayo anayang’ana phewa la Coyotito ndipo kenako anayamba kumukoka zikope kuti awone m’maso. “Zikuchitika ndendende mmene ndimaganizira,” anatero doko- talayo. “Poyizoni wambiri adakali m’thupi la mwanayu. Tabwera udzawone!” anatero dokotalayo akukoka chikope cha Coyotito ngati akusenda nthochi. “Wawona, masowatu ayamba kale kuwoneka abu- luwu.” Masowo ankawonekadi abuluwu pang’ono. Komabe, Kino sankadziwa ngati masowo ankawoneka choncho nthawi zonse kapena ayi. Chomwe ankafuna chinali choti mwana wake achire basi. “Ndimupatsa mankhwala oti achotse poyizoni amene watsalirayu,” anatero dokotalayo akupereka mwanayo kwa Kino. Kenako anatulutsa kabotolo kamankhwala enaake oyera. Ndiyeno analandiranso mwana uja n’kumutsegula kukamwa n’kumupungulira mankwalawo kukhosi. Atatero anasendanso chikope cha mwanayo n’ku- mamuyang’ana m’maso mokhala ngati akufuna kuwona ngati mankhwala wamumwetsawo afika pamene amayenera kulowa. Patapita kanthawi, anapereka mwanayo kwa Juana. Kenako anate - 22