Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale 2 | Page 19

Ngale yakuti, kamwala kankalowa m’chikamba chankhono ndipo nkhonoyo inkayamba kukuta mwalawo ndi zinazake zolimba. Mkupita kwa nthawi kamwalako kankasanduka ngale. Ngale zina zinkakhala zazing’ono kwambiri moti anthu ankazigulitsa pamtengo wolira. Koma anthu amphumi ankatha kupeza ngale yayikulu komanso yokongola yomwe akayigulitsa ankakatamuka kwambiri. Kwa zaka zochuluka, aso- dzi ankasakasaka ngale m’nyanjayi. Koma kunena zowona, kupeza ngale yabwino unkakhala mwayi wawukulu. Kalekalelo, panyanjayi pankapezeka ngale zochuluka zedi. Ngalezi ndi zimene zinachititsa kuti mfumu ya ku Spain ilemere. Tikutero chifu- kwa inkakwanitsa kulipira asilikali ake ndi ndalama zomwe inkapeza kuchokera ku ngale zomwe zinkapezeka m’derali. Mapeto ake, mfumuyi inakhala yamphamvu kwambiri. Choncho, anthu ankalowa m’nyanjayi n’kumakafufuza nkhono zokhala ndi ngale ndipo akazipeza ankazikanula n’kuyang’ana mkati mwake ngati muli kanthu. Kino anavula zovala komanso chisoti chake n’kuziponya m’bwato. M’manja mwake munali zingwe ziwiri. Chingwe china chinamangidwa kumwala ndipo china chinamangidwa kuthumba. Kenako anagwira mwalawo m’dzanja lake limodzi komanso thumba lija m’dzanja lina, n’kulumphira m’nyanja. Mwalawo unamuthandiza kuti asavutike kukafika pansi. Ankati akayang’ana kumwamba ankawona dzuwa liku- walitsa nyanjayo ngati galasi komanso bwato lawo lija likuyandama. Kenako anayamba kusambira pang’onopang’ono kuti asavundule matope omwe anali pansi pa nyanjayo. Manja ake ankagwira ntchito yayikulu zedi. Iye ankatolera nkhono n’kumaziyika m’thumba anatenga lija. Monga tanenera kale, anthu a mtundu wa Kino ankayimba nyimbo zokhudza chilichonse chimene maso awo awona. Iwo ankapeka nyimbo zonena za nsomba, mafunde, kuwala, mdima, dzuwa komanso mwezi. Nyimbo zimenezi zinalinso m’mutu mwa Kino. Pamenepatu tikunena za nyimbo iliyonse yomwe inapekedwa, ngakhalenso zimene zinayiwalid- wa. Choncho pamene ankatolera nkhono zija, nyimbo inkamveka m’mu- tu mwake. Komano mkati mwa nyimbo imeneyo munalinso kanyimbo kena kachinsinsi. Imeneyi inali Nyimbo ya Chiyembekezo. Kodi m’zi- 13