Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale 2 | Page 15

Ngale ndi anthu a mtundu wa Kino, ankangokhala ngati akuyankhula ndi agalu. Koma ataganizira mkazi wake Juana, Kino analimba mtima ndipo anachotsa chisoti chake n’kuyamba kugogoda. Pa nthawiyi, Coyotito anali atayambiranso kulira ndipo Juana ankamutonthoza. Aliyense anadikirira kuti awone chozizwitsa. Patapita kanthawi pang’ono, geti lija linatsegulidwa pang’ono. Mu- nthu amene anasuzumira pagetipo anali wamtundu wake. Kino anaya- nkhula naye m’chinenero chamakolo. “Tikufuna tiwonane ndi dokotala,” anatero Kino. “Mwana wanga walumidwa ndi pheterere.” Atangomva zimenezi, watchitoyo anatseka geti. Zikuwoneka kuti sankafuna kuyankhula m’chinenero chamakolocho, Chiyindiya, chomwe ankachitenga kuti ndi cha anthu osazindikira, anthu omwe ankayenda manthongo ali bwito-o m’maso. “Dikirani pang’ono ndikawawuze,” anatero wantchitoyo m’Chi- sipaniya kwinaku akumalizitsa kutseka gelilo ndi chitsulo kuti pasa- pezeke wina wochita chipumi bibibi n’kumasuzumira kumpandako. M’mawawu kunja kunkatentha monyansa moti dzuwa lomwe linafu- tukuka ngati mafuri linkachititsa kuti zithunzithunzi za anthuwo ziziwoneka pageti komanso pakhoma lampandawo. Dokotalayo anali atakhala pakama wake kuchipinda. Iye anali akungodzuka kumene. Anali atavala chijasi chake chapogona chopa- ngidwa ndi nsalu yabafuta. Chijasicho chinali chochokera ku Paris. Pa nthawiyi anali atamanga mabatani onse moti chifukwa cha kukula mi- mba, ankangowoneka ngati mbululu, kapena mzimayi wapakati. Doko- talayu anali akumwa tiyi wake yemwe anali m’kapu yodula kwambiri yochokera ku China. Pambali pake panali tebulo lomwe anayikapo kabe- lu kachikalekale ndiponso kambale kozimitsira fodya. Makatani ko- manso makabati omwe anali m’nyumbamo ankachititsa kuti mukhale chimdima. Munalinso zithunzi zachipembedzo komanso chithunzi chachikulu cha mkazi wake yemwe anamwalira zilumika zapitazo. Dokotalayu anapanganso kapu ina ya tiyi n’kumamwera bisiketi 9