Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale 2 | Page 12

Ngale pheterere. Ankadziwa kuti munthu wamkulu amagona pamphasa kwa masiku ambiri chifukwa cha ululu wapheterere. Koma ankadziwanso kuti akakhala mwana mpamene zimakhalanso zowopsa kwambiri chifu- kwa kupanda kusamala akhoza kukumwalirirani m’manja. Zomwe zinkachitika ndi zoti ankayamba ndi kutentha thupi, kenako ankalephe- ra kupuma. Pamapeto pake ankayamba kumva kupweteka m’mimba zomwe zinkatsatana ndi kusanza. Mukapanda kumupatsa chithandizo cholongosoka, mwanayo ankagona tulo tosadzukanso. Izi ndi zimenenso zikanachitika ndi Coyotito akanapanda kuthamangira naye kwa doko- tala mwansanga. Ngakhale Juana anakwanitsa kutsopapo poyizoni wina, zikuwoneka kuti anali atafalikira kale. Komabe ululu unali utayamba kuchepa moti Coyotito anatonthola. Kino ankadabwa kwambiri ndi kupirira kwa mkazi wake. Kunena zowona Juana ankawoneka ngati wosalimba. Koma chilungamo chake ndi chakuti anali chitsulo. Analinso ndi makhalidwe abwino monga kumvera komanso kugonjera. Mwachidule tinganene kuti ankachita zonse zimene Kino ankafuna popanda kuwiringula kapena kunyinyiri- ka. Analinso wawulemu, wolimbikitsa komanso wodekha. Juana anali dalitso lalikulu kwa mwamuna wosawuka modetsa nkhawa ngati Kino. Anali wolimbikira ntchito zedi ndipo nthawi zina ankachita zimenezi kumimba kuli pululu. Zikuwoneka kuti anali wopirira ndi njala, mwinanso kuposa mwamuna wake. Akadwala, ankadzilimbitsa n’kumagwirabe ntchito ndipo sankafuna dokotala. Koma patsikuli anachita zinthu zachilendo. “Dokotala,” anatero Juana. “Pitani mukayitane dokotala.” Anthu aja anapatsiranapatsirana uthengawo mpaka onse anamva zoti Juana akufuna dokotala. “Juana akuti akufuna dokotala,” ankanong’onezana motero anthuwo. Zimenezi zinali zodabwitsa kwambiri. Kunena mosapsatira, kwa an- thuwa chinali chozizwitsa kuyitana dokotala n’kubweradi. Zinalinso zachilendo ngakhale kufuna dokotalako. Kuti dokotala abwere kunyum- ba zawudzuzi pankafa m’mwenye. Dokotala sankabwera kunyumba za anthu osawuka, omwe analibe kalikonse koti angamupatse. Komanso, 6