Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 99

Miyambi ya Patsokwe chathadi tisananena kuti tamaliza. Kumanga nyumba panjira n’kumangira alendo. -Apaulendo samatha pakhomo pako ukamanga m’mbali mwa msewu, amabwera kudzapempha malo ogona. Kumanga sumanga kawiri. -Pali zinthu zina zomwe zimafunika kuzichita kapena kugwiri- zana kamodzi kokha monga kumanga banja. Kumangitsa madzi m’masamba. -Nthawi zambiri anthu sasunga malonjezo. Akachita zimenezi amakhala ngati akumangitsa mnzawoyo madzi m’masamba kapena kuti amupusitsa. Kumangitsa madzi m’mayani. -Nthawi zambiri anthu sasunga malonjezo. Akachita zimenezi amakhala ngati akumangitsa mnzawoyo madzi m’masamba kapena kuti amupusitsa. Kumawerengera mtengo wake. -Mawuwa anachokera ku zimene Yesu ananena zoti, “Ndani amene amene akafuna kumanga nsanja sayamba wakhala pansi ndi kuwerengera mtengo wake?” Ndi bwino kumakonzekera tikafuna kuchita chinthu kuti tisachilephere anthu n’kutiseka. Kumayenda kuti uwone agalu amichombo. -Ukayenda m’madera ena a dziko umaona zinthu zachilendo. Si bwino kungokhala pamodzimodzi. Kumayenda kuti uphunzire zinthu. Kumbire adamka nawo kumanda. -Si bwino kuzolowera kuchitiridwa chinthu chifukwa udzavuti- ka amene amakuchitirawo akadzachoka kapena kumwalira. Kumbire adanka nawo. -Tisamadalire munthu m’modzi yekha. Ndi bwino kugawanako 98