Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 98
Miyambi ya Patsokwe
Kumana anzako n’kudzimana wekha.
-Ukathandiza mnzako umakhala ngati wadzala, mawa
adzakuthandiza iweyo.
Kumana n’kubisa.
-Si bwino kumanamiza ena.
Kumana n’kudzipha.
-Ukathandiza mnzako umakhala ngati wadzala, mawa
adzakuthandiza iweyo.
Kumanda kulibe chisoni.
-Kumanda kumatenga aliyense, kaya ndi mphawi, wamkulu
kapena amene sanalidyerere dzikoli.
Kumanda kumapita anthuanthu, n’kusiya zitsiru.
-Anthu abwino sakhalitsa padzikoli.
Kumanda sankira dumbo.
-Mawuwa amatanthauza kuti tikakhala pamavuto tisamaloze
ena chala kuti ndi amene akuchititsa.
Kumanda sikupita mtolo wa udzu, kumapita mtembo wa mun-
thu.
-Kaya munthu amachita zabwino chotani, tsiku lina adzamwali-
ra n’kupita kunsabwerera.
Kumanga khobwe ndi m’mawa.
-Pofuna kuchita zinthu ndi bwino kuzichita mopanda chidodo
kapena mosachedwa.
Kumanga mlaza m’maso.
-Pofuna kukwatira pamafunika kulimba mtima. Umafunika ku-
khala ngati wamanga nsalu m’maso kuti usachita manyazi.
Kumanga mwamanga, koma anyamkalere.
-Anyamkalere ndi timaulusi tomwe timangoti balalabalala mun-
thu akamanga zinazake. Tiyenera kuonetsetsa kuti chilichonse
97