Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 97
Miyambi ya Patsokwe
zosakhala zenizeni.
Kulinda mdima ndi nthanthi zako.
-Nthanthi ndi nkhani kapena nthano. Mawuwa amanena za
munthu amene akungonena nkhani mozungulira mpaka mdima
kugwa. Tikamanena zinthu ndi bwino tizipewa kunena nkhani
mozungulira. Ndi bwino kumangotumbula.
Kulinji akudza ndi njira.
-Tikamakhala tizikonzekera chilichonse. Zinthu zimatha kusin-
tha mwadzidzidzi.
Kulirira kuutsi.
-Mawuwa amanenedwa ngati wina wakumana ndi mavuto
chifukwa chosamva ndiye akuyesa kuphumba anthu m’maso
kuti asadziwe kuti akuvutika chifukwa cha kusamvako. Ama-
khala ngati wakhala pamene pali utsi kuti anthu aziti akulira ndi
utsiwo, chonsecho akulira chifukwa cha ululu.
Kuliza ng’oma yowambawamba.
-Mawuwa amanenedwa ngati wina wachita zimene ena ama-
yembekezera. Kapena ngati wachita zinthu zimene enanso ama-
funa. Mwachitsanzo, mkazi amene wafunsiridwa zili zoti nayen-
so amamufuna angavomere poyankha mwamanyazi kuti,
“Mwayimba ng’oma yowambawamba.”
Kuloza ndi chala.
-Mawuwa amanenedwa ngati munthu wina anachita zinthu
zomwe zamubweretsera mavuto monga kuba kapena kuchita
mwano.
Kulumpha dzenje n’kulionera patali.
-Vuto silivuta kuthana nalo ngati walionera patali. Ndi bwino
kumakonzekera tisanakumane ndi mavuto.
96