Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 96
Miyambi ya Patsokwe
Kulaula n’kuzula m’mera.
-Mawuwa amanenedwa munthu akayankhula mosabisa mawu
kapena kuti mwatchutchutchu.
Kulawa kumatha mphika.
-Osamakhala munthu wokomedwa ndi zinthu chifukwa ukhoza
kukumana ndi mavuto.
Kulemera ndi kudya, ukavala malaya akubera.
-Palibe amene angakulande chimene wadya, choncho kulemera
ndi mmene umadyera osati zinthu zimene anthu ena akhoza ku-
kubera n’kukhala zawo.
Kulemera ndi kudya.
-Kudya bwino n’kumene kungasonyezedi kuti munthu ndi
wolemera. Palibe amene adzalowe m’manda ndi katundu. Aku-
ba akhoza kukubera katundu wako koma sangakubere chimene
chalowa m’mimba.
Kuli zii, azimu adutsa.
-Anthu akangoti zii amati azimu adutsa chifukwa safuna phoko-
so. Mawuwa anayamba chifukwa cha zikhulupiriro zoti kunja
kuno kuli mizimu.
Kulibe manda a mbeta.
-Aliyense amakaikidwa kumanda akamwalira. Choncho,
tisamade nkhawa ena akamatinena kuti timwalira tisanakwa-
tiwe kapena kukwatira.
Kulimana pamsana.
-Mawuwa amatanthauza kuchenjeretsana. Akakhala kuti amene
wachenjeretsedwa ndi mmodzi, amati amulima pamsana.
Kulimbikira mtunda wopanda madzi.
-Mawuwa amatanthauza kulimbikira kuchita zinthu zomwe
sungaphulepo kanthu. Angatanthauzenso kuwerengera zinthu
95