Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 95
Miyambi ya Patsokwe
akamuthamangitsa uku amapita kwinako. Koma banja loteroro
limakhalanso ndi mavuto osaneneke monga nsanje komanso
kusasonyezedwa chikondi chokwanira.
Kukwatira mkazi wokongoka n’chimodzimodzi kudzala
mtengo wamango m’mbali mwa njira.
-Mavuto amene wakwatira mkazi wokongola ndi munthu ame-
ne wadzala mtengo wamango m’mbali mwa njira, amafanana
chinthu chimodzi: Onse amavutika ndi anthu akuba!
Kukweza bankha patsekera.
-Munthu sungakweze bankha patsekera, likhoza kuthyoka.
Munthu wamkulu asamachite zibwana kapena kumasewera ndi
ana.
Kulamula Vumbwe n’kulinga uli ndi Nkhukhu.
-Munthu usamapalamule kapena kuputa dala mavuto ulibe
pothawira. Kuti ulamulire anthu umayenera kukhala ndi ndala-
ma kapena mphamvu.
Kulanda mwana n’kudyetsa.
-Munthu ungathe kutenga ndi kulera mwana ngati un-
gakwanitse kumudyetsa bwino.
Kulanga nyani n’kuphwanya mutu.
-Poweruza mlandu, si bwino kumawiringula. Umafunika
kunena cholakwa chenicheni chimene munthu wachita. Ukatero
zimakuyendera.
Kulasa mtengo n’chamuna chomwe.
-Mlenje wina anaphonya Njati n’kukhapa mtengo. Ngakhale
anaphonya, komabe anachita chamuna ndithu. Ndi bwino kuti
nafenso tiziyesetsa kuchita khama pochita zinthu, zizichita
kukanika zokha.
94