Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 94
Miyambi ya Patsokwe
sanaitanidwe angatsatire, choncho woitanayo amanena kuti,
“Ndakhululukira mamina a fodya.” Mwambiwu ungatan-
thauzenso kuti kanthu kakang’ono kakhoza kubweretsa mavuto
aakulu.
Kukoma kwa dziko n’kulinga utakhalako.
-Kukhala ndi umboni weniweni wa chinthu n’kulinga utachiona
komanso kukhala nacho.
Kukoma kwa mnzako ndi kamba wako.
-Kuti munthu udziwe khalidwe la munthu, umafunika kungo-
yang’ana amene amacheza nawo. Munthu ukhoza kuweruzidwa
chifukwa cha khalidwe la anzako. Mbiri yako ikhoza kuipa
kapena kukoma chifukwa cha amene umayenda nawo.
Kukoma ndi kuwonjezera.
-Zinthu zimakongola kapena kukhala bwino kwambiri
ukamazikongoletsa kapena kuziwonjezera.
Kukondwa ndi kuonetsa mano.
-Kusangalala kwenikweni kumaoneka. Pali ena omwe amasek-
erera n’kumaoneka ngati adya tsabola.
Kukula mphuno sikudziwa kumina.
-Kuchenjeretsa sikusonyeza kuti munthu amadziwa zonse.
Kukula mutu si nzeru.
-Nzeru zenizeni zimaoneka ndi zosankha za munthu, osati
chifukwa choti anabadwa kale kapena ndi wamkulu mutu.
Kukula saimbira maseche.
-Munthu asamadikire kuti ena achite kumuuza kuti wakula.
Ayenera kusintha yekha n’kumachita zinthu ngati wamkulu.
Kukwatira chiwiri kudakoma.
-Chinthu chilichonse chili ndi poipira ndi pabwino pake.
Mwachitsanzo, munthu amene wakwatira chiwiri, amati
93