Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 93
Miyambi ya Patsokwe
kuti wachita bwino. Iye angayankhe modzichepetsa kuti,
“Kukana nsalu ya akulu n’kuviika.” Akuluakulu akatituma, si
bwino kukana koma kungochita zomwe tingathe.
Kukankha konjuta.
-Mawuwa amanena za munthu amene akupereka chifukwa
chosamveka bwino chomwe walepherera kuchita zinazake.
Kukhala awiri si mantha.
-Anthu akakhala awiri amatha kuchita zinthu modalirana ndipo
amatha kuthandizana wina akapeza mavuto.
Kukhala kumunda n’kuona ndime.
-Osamangodzichemerera ndi pakamwa pokha, koma anthu
aziona ntchito za manja athu.
Kukhala kwa eni n’kuomba m’manja.
-Munthu ukakhala kwa eni umayenera kumalemekeza anthu
amene wawapeza.
Kukhala kwa eni ndi kuweteka.
-Munthu ukakhala kwa eni umayenera kufatsa. Ukamachita
matukutuku amakuthamangitsa.
Kukhala m’chiluli n’kuyambirira.
-Mawu akuti kukhala m’chiluli akutanthauza kukhala ndi zo-
chuluka. Tisamazengereze tikafuna kuchita kanthu.
Tisamachedwe pochita zinthu.
Kukhala owolowa manja n’kulinga uli ndi kanthu.
-Munthu yemwe alibe kalikonse sangagawire ena zinthu, nanga
azitenga kuti?
Kukhululukira mamina a fodya.
-Anthu amene amafwenkha fodya, amatha kufwenkhera limodzi
ndi mamina n’kuwakhululukira chifukwa cha fodyayo. Pamene
munthu waitana munthu m’modzi yekha, ambiri amene
92