Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 92

Miyambi ya Patsokwe Kuipa khope kumaombola. -Kusakhala wokongola kumapangitsa kuti upewe mavuto ena. Mwachitsanzo, mtsikana akhoza kumaliza sukulu chifukwa choti anthu sankakufunsirafunsira. Kuipa satsanzirana. -Si bwino kumatsanzira anzako akamachita zoipa. Kuipira mduliro mutu uli wako. -Pali ena omwe amadulira tsitsi lawo n’kupezeka kuti sakuon- eka bwino. Mwambiwu umatanthauza kuti nthawi zambiri an- thufe timaipitsa zinthu zathu zomwe zinali zokongola poganiza kuti zikongola kwambiri. Kuiwala kulibe mankhwala. -Kuiwala n’kosapeweka. Kukana chimbudzi n’kuvomera mikodzo. -Mwambiwu umanenedwa munthu akamakana chinthu chom- we chili ndi umboni wodziwikiratu. Kukana kali kutsaya. -Mawuwa amanenedwa ngati munthu akukana zinthu zomwe akudziwa kuti wachita. Nthawi zinanso ena amakana pali um- boni wooneka bwino woti achita chinthucho ndi iwowo. Kukana kwam’tuwagalu. -Mawuwa amatanthauza kukanitsitsa. Kukana nsalu ya akulu nkuviika. -Mawuwa amanena za mwana wamwano, yemwe wangolandira nsalu ya munthu wamkulu kuti aichapa koma iyeyo n’kungoiviika. Atamufunsa ngati wachapa anawalozera nsalu yomwe wangoviikayo kuti wachapa. Mawuwa angagwirenso ntchito kwa munthu wodzichepetsa, anthu akamamuyamikira 91